PEMPHERO LOKAKAMIZA LALITALI
Iye amene afuna kunena Pempheroli, ayenera kuyimirira ndipo atembenukire kwa Mulungu, ndipo poimirira pamalo akewo, iye ayang’ane kudzanja lamanja ndi lamanzere, ngati kuti akuyembekezera chifundo cha Ambuye Wake, Wachifundo-Choposa, Womvera Chisoni. Tsono iye anene kuti:
O Inu Amene muli Ambuye wamaina onse ndi Mlengi wa miyamba! Ndikupemphani Inu kubzolera mwa iwo Amene ali kasupe a Uweniweni Wanu osaonekawo, Wokwezeka koposa, Waulemelero Onse, kuti mulipange pemphero langa, moto umene uwotche zophimba zimene zanditseka ine kuti ndisaone kukongola Kwanu, ndi kuwala kumene kunditsogolere ine ku nyanja ya kumene Inu Mukupezeka.
Kenaka iye akweze manja ake mopempha kulozera kwa Mulungu -wodalitsika ndi wokwezeka ndi Iye – ndipo anene:
O Inu Khumbo la dziko lapansi ndi Okondedwa wa amitundu! Inu mukundiwona ine ndikutembenukira kwa Inu, ndikudzilekanitsa kwa aliyense kupatula Inu, ndi kukakamira ku chingwe Chanu, chomwe kubzolera mu mayendedwe ake chilengedwe chonse chawongoleredwa.
Ndine mtumiki Wanu, O Ambuye wanga ndiponso mwana wa mtumiki Wanu. Onani ine ndili chilili kukonzekera kuchita Chifuniro Chanu ndiponso khumbo Lanu, ndi kusafuna china chilichonse kupatula chikondwerero Chanu chokoma. Ndikudandaulirani kubzolera m’nyanja ya chifundo Chanu ndi Nyenyezi ya Nthanda ya chisomo Chanu kuti muchite naye mtumiki Wanu monga momwe mufunira ndi kusangalatsidwira. Mwa nyonga zanu zomwe zili patali popitilira kutchula konse ndi chitamando chilichonse! Chimene chaululidwa ndi Inu ndikhumbo la mtima wanga ndiponso chokondedwa cha moyo wanga. “O Mulungu, Mulungu wanga! Musaone zimene ndifuna ndi zochita zanga koma muone chifuniro Chanu zimene zakutila kumwamba ndi pansi pano. Mu Dzina Lanu Lalikulu Lopambana kwambiri, O Inu Ambuye wa mafuko onse! Ndikufuna zokha zimene Inu mufuna, ndipo zokha zimene Inu Mukonda.”
Kenaka iye agwade, ndikugwetsa mphumi yake pansi, anene kuti:
Okwezeka Muli Inu pamwamba pa chifotokozo cha wina aliyense kupatula Inu nokha, ndi kuzindikirika ndi kena kalikonse kupatula Inu.
Kenaka ayimilire ndi kunena:
“Pangani pemphero langa, O Ambuye wanga, mtsinje wa madzi a moyo pamene ndingathe kukhala moyo wautali monga m’mene ufumu Wanu ungakhalire, ndipo
ndingathe kutchula Inu mudziko liri lonse la Maiko Anu." Kenaka iye akwezenso manja ake mopempha, ndipo anene:
O Inu amene polekanitsidwa Nanu mitima ndi miyoyo yosungunuka, amenenso ndi moto wa chikondi Chake dziko lonse lapansi layatsidwa! Ndikudandaulira Inu mwa Dzina Lanu kubzolera mwa lomwe Inu mwagonjetsa chilengedwe chonse, musandimane ine chimene chilli ndi Inu, O Inu Amene mulamulira anthu onse! Inu mukumuona, O Ambuye wanga, mlendoyu kuthawira kwawo kokwezeka kopambana pansi pa chophimba cha ufumu Wanu, ndi cholengedwa chosaukachi kasupe wa chuma Chanu. Yanu ndi mphamvu yolamulira chilichonse chomwe Inu mufuna. Ndichitira umboni kuti Inu muyenera kutamandidwa mu zochita Zanu, ndi kukumverani mu chilamulo Chanu, ndi kukhalabe osakakamizidwa mu ulamuliro Wanu.
Kenaka a kweze manja ake ndi kunena Dzina Lalikulu (Alláh-u-Abhá) katatu.
Kenaka aweramire pansi manja ali pa maondo pamaso pa Mulungu – wodalitsika ndi okwezeka akhale Iye – ndi kunena:
Inu mukuona, O Mulungu wanga, momwe mzimu wanga wagwedezekera mkati mwa nthiti ndi ziwalo zanga, mkufunitsitsa kwake kuti ukupembedzeni Inu, ndi mkulakalaka kwake kuti ukukumbukireni Inu ndi kukulemekezani Inu; momwe ukuchitira umboni mu ufumu wa chinenero Chanu ndi kumwamba kwa Nzeru Zanu. Ndikonda mu khalidwe limeneli, O Ambuye wanga, kupempha kwa Inu zonse zimene muli nazo, kuti ndilangize umphawi wanga, ndi kukulitsa chaulere Chanu ndi chuma Chanu, ndi kulengeza kufooka kwanga, ndi kuvumbula mphamvu Zanu ndi Nyonga Zanu.
Kenaka iye ayimirire ndi kukweza manja ake kawiri mopempha, ndi kunena:
Kulibe Mulungu wina koma Inu, Wamphamvu zonse, wachaulere Chonse. Kulibe Mulungu koma Inu, mkozi, poyamba ndi pomaliza pomwe. O Mulungu, Mulungu wanga! Chikhululuko Chanu chandilimbikitsa, ndipo kuyitana kwanu kwandidzutsa, ndipo chisomo chanu chandikweza ndi kunditsogolera kwa Inu. Ndine yani, kuti ndingathe kulimba mtima kuti ndiyimilire pachipata cha mzimu woyandikira Nanu, kapenanso kulodzetsa nkhope yanga ku nyali zomwe zili kuwala kuchokera kumwamba kwa chifuniro chanu? Inu mukuona, O Ambuye wanga, cholengedwa chochititsa chisonichi chikugogoda pakhomo lachisomo Chanu, ndi moyo wakuthawu ukufunafuna mtsinje wamoyo osatha kuchokera kumanja a chaulere Chanu. Chanu ndi chilamulo nthawi zonse, O Inu Amene muli Ambuye wa maina onse, ndipo kwanga ndi kusawiringula ndi kugonjera malolera ku chifuniro Chanu, O Mlengi wa miyamba!
Kenaka iye akweze manja ake katatu ndi kunena:
Wamkulu ndi Mulungu kuposa wamkulu aliyense!
Kenaka iye agwade ndi kugwetsa mphumi yake pansi, ndi kunena:
Muli apamwamba zedi Inu kukutamandani kwa iwo amene ali pafupi Nanu kuti afike kumwamba pafupi Nanu, kapena mbalame za mitima ya iwo amene ali odzipereka kwa Inu kuti afikedi pa chitseko cha chipata chanu. Ndichitira umboni kuti Muli opatulika pamwamba pa zizindikiro zonse, ndiponso Woyera pamwamba pa maina onse. Palibe Mulungu wina koma Inu, wopambana koposa onse, wa Ulemerero onse.
Kenaka akhazikike pansi ndi kunena:
Ndichitira umboni ku chimene zolengedwa zonse zachitira umboni, ndi makamu a kumwamba, ndi okhala mu Paradizo Okwezeka koposa, ndipo kuseri kwaoko lilime la ulemelero ili lomwe kuchokera ku malekezero a ulemelero onse, kuti Ndinu Mulungu, kuti kulibenso Mulungu koma Inu, ndipo kuti Iye Amene wavumbulutsidwa ndi chinsinsi chobisika, chizindikiro chosungidwa, kubzolera mwa Amene malembo B ndi E (kukhala) aphatikizana ndi kulukana pamodzi. Ndichitira umboni kuti ndi Iyeyo Amene dzina lake lalembedwa ndi Cholembera cha Wamwambamwamba, ndinso Amene watchulidwa mu Mabuku a Mulungu, Ambuye Wampando wa Chifumu m’mwambamo ndi pansi pano. Kenaka ayimilire njo ndi kunena:
O Ambuye wa zolengedwa zonse ndi mwini wa zinthu zonse zooneka ndi zosaoneka! Inu mukuiona misozi yanga ndi zisisimo zomwe ndikunena, ndi kumvetsera ku kubuula kwanga, ndi kuchema ndi chiliro cha mtima wanga. Ndi nyonga Zanu! Zolakwa zanga zanditsekerezera kumbuyo kuti ndisayandikire Nanu; ndipo machimo anga andiyimitsa kutali kuchokera kubwalo la milandu la chiyero Chanu. Chikondi Chanu, O Ambuye wanga, chandilemeza ine, ndipo malekano ndi Inu yandiononga ine, kutalikirana ndi Inu kwandidya ine.
Ndikupemphani Inu ndi mayendedwe Anu mu chipululuchi, ndiponso ndi mawu “Ndili pano, Ndili pano” amene osankhidwa Anu adalankhula mu ufumu Wanu, ndi mpumo wa Chibvumbulutso Chanu, ndi mphepo zodekha za kudza kwa Mbandakucha wa Mbvumbulutsi Wanu, kukonza kuti ndiyang’anire pa kukongola Kwanu ndi kutsata chilichonse chomwe chilli mu Bukhu Lanu.
Kenaka iye anene Dzina Lalikulu (Alláh-u-Abhá) katatu ndi kuweramira pansi manja ali pa maondo, ndi kunena:
Mayamiko akhale kwa Inu, O Mulungu wanga, pakuti Inu mwandithandiza kukumbukira Inu ndiponso kukuyamikani Inu, ndipo mwandizindikiritsa ine Iye Amene ali Mbandakucha wa Zizindikiro Zanu, ndipo mwandipangitsa kuweramira pansi pamaso pa Umbuye Wanu, ndi kudzichepetsa pamaso pa Umulungu Wanu, ndi kuvomereza chimene chayankhulidwa ndi lilime la ukulu wanu.
Kenaka iye aweramuke ndi kunena:
O Mulungu, Mulungu wanga! Msana wanga wawelama ndi kulemedwa kwa machimo anga, ndipo kusasamala kwanga kwandiononga ine. Ndikamaganizira kuipa kwa zochita zanga ndi chisamaliro Chanu, mtima wanga usungunuka mkati mwanga, ndipo magazi anga akuwira mkati mwa misempha yanga. Mwa kukongola Kwanu, O Inu khumbo la Dziko lapansi! Ndili ndi manyazi kukweza nkhope yanga kwa inu, ndipo manja anga olakalaka ali ndi manyazi kutambasukira kuloza kumwamba kwa chaulere Chanu. Inu mukuona, O Mulungu wanga, momwe misozi yanga ikundilepheretsa kukumbukira Inu ndi kukuza zabwino Zanu, O Inu Ambuye Wampando wa Chifumu m’mwambamo ndi dziko lapansi pano!
Ndikudandaulirani mwa zizindikiro za Ufumu Wanu ndi zodabwitsa za ulamuliro Wanu kuchita ndi okondedwa Wanu monga kuyenera chaulere Chanu, O Ambuye wa zamoyo zonse, ndipo muyeneradi chisomo Chanu, O Mfumu ya zooneka ndi zosaoneka!
Kenaka iye anene Dzina lalikulu (Alláh-u-Abhá) katatu ndi kugwada mphumi yake ili pansi ndi kunena:
Mayamiko akhale kwa Inu, O Mulungu wathu, pakuti Inu mwatitumizira ife chomwe chatisendeza m’fupi ndi Inu, ndipo mutipatse ife chabwino chilichonse chotumizidwa ndi Inu mu Mabukhu Anu ndi Malembo Anu. Titetezeni, tikupemphani Inu, O Ambuye wanga, ku makamu a malingaliro a zinthu zopanda pake, ndi maganizo achabe.
Inu, ndithudi, Ndinu Wanyonga, Wodziwa Zonse.
Kenaka awutse mutu wake ndikukhazikika pansi ndi kunena:
Ndichitira umboni, O Mulungu wanga, kuchimene osankhidwa Anu achichitira umboni, ndi kuvomereza chimene okhala ku Paradizo okwezekayo ndi iwo azinga mozungulira mpando Wanu Wamphamvu achivomereza. Maufumu adziko lapansi ndi kumwamba ndi Anu, O Ambuye wa maiko!