Ridván Messages
Chichewa · Universal House of Justice
Nkhani ziwiri zomwe zangochitika zatipangitsa ife kuti tigawane nanu mawu awa. Nkhani yoyamba ndi yokhudza mliri woopsa ndi osowetsa mtendere wa Corona omwe wakolera padziko lonse lapansi. Mmaiko ambiri, pambali pa kuyesetsa ndi khama kwa anthu limodzi kulimbana ndi vutoli, zotsatira zafika kale pachiopsezo, ndipo maanja ndi anthu akhudzidwa ndipo dziko lili pa mavuto. Mafunde a mazunzo ndi chisoni akufalikira dera ndi dera, ndipo izi zifooketsa maiko osiyana-siyana, pa nthawi zosiyana, munjira zosiyana-siyananso.
Nkhani yachiwiri, yomwe tsiku ndi tsiku ikuonekera, ndi kulimba mtima ndi kuchilimika kwa dziko lachiBaha’i mu nthawi ya msautsoyi yomwe sitingayifanirize ndi chilichonse. Kuyesetsa kwanu kwakhala kwa pamwamba. Pomwe tinakulemberani mwezi wapitawo pa Naw-Ruz, tinali ndi chidwi kutsindika za makhalidwe abwino omwe mbumba zomwe patani yawo ya kachitidwe kazinthu inasokonekera, zikuonetsa. Zonsezi zapangitsa mu sabata zotsatira, zimene abwenzi ochuluka anali kutsatira malamuo okhwima oyikidwa, kuzamitsa chiyamikiro chathu. Kuphunzira kochokera mbali zina za dziko lonse, mbumba zina zapeza njira zotetezeka ndi zabwino zobweretsa chidziwitso pa nkhani zaumoyo zofunikira kuzidziwa. Chidwi chachikulu chikuperekedwa kwa omwe ali pachiopsezo chachikulu ku nthendayi ndi zovuta zobwera ndi kufalikira kwa kachilomboka maka pankhani za chuma; kuyesetsa komwe akuchita ofalitsa nkhani pa makina a intaneti a Nkhani zokhudza a Baha’i padziko lonse (Baha’i World News Service) ndi chitsanzo chimodzi chabe mwa zambiri zomwe zili mkati. Izi zikuthandizidwa ndi kuyesetsa kopanga kafuku-fuku, kutukula ndi kubweretsa pamodzi makhalidwe auzimu amene ali ofunikira panthawi ino. Kuyesetsa kochuluka kotere kukuchitika pa banja kapena pawekha, koma pomwe pali kuthekera ndipo kulumikizana ndi kotheka, khalidwe lothandizana ndi kubwera pamodzi likupititsidwa patsogolo pakati pa anthu omwe ali mu vuto lofanana. Moyo wotaka-taka wa mbumba, ofunika kwambiri pa kupita patsogolo kwa dera sulepheretsedwa.
Mizimu yathu yalimbikitsidwa poona momwe maBungwe Auzimu Aakulu mothekera, atsogoleri a Wankhondo wa Kuwala atsogolera mbumba ndi kuthandiza kukonzekera bwino kuchitapo kanthu pa vutoli. Iwo athandizidwa molimba ndi Alangizi ndi Athandizi awo amene, monga mwa nthawi zonse, awonetsa moonadi mtima mlingo wa kutumikira mwachikondi. Pomwe akukhala odziwitsidwa bwino za kusintha komwe kukuchitika mmaiko awo, Mabungwe akonza zonse zofunikira zokhudza ntchito za kayendetsedwe ka Chipembedzo, maka pa nkhani ya masankho, ku malo komwe kuli ndi kuthekera. Kudzera mu kulumikizana kwapafupi-fupi, zikhazikitso ndi makomiti apereka ulangizi wanzeru, kupereka chitsimikizo ndi chilimbikitso pafupi-pafupi. Nthawi zambiri, ayambanso kufufuza mfundo zomanga zimene zikuyamba kuonekera mu zochitika za m’madera. Chiyembekezo chimene tidapereka mu uthenga wathu wa Naw-Ruz kuti mayesero awa akupilira kwa mtundu wa anthu adzapereka kuzindikira kwakukulu kwayamba kale kuoneka. Atsogoleri, anthu oganiza bwino ndi opereka malipoti ayamba kufufuza mfundo zokhazikika ndi zokhumba zachindunji kuti, mu nthawi ya posachedwa, zakhala zikusowa kwambiri mu ntchito zam’dera. Mu nthawi ino izi zilingati kuthwanima koyambilira, komabe zikuonetsa kuthekera kuti nthawi ya kukhudzika kwa pamodzi kutha kukhala kwayandikira.
Mtidzi omwe tili nawo poona kuchilimika kwa dziko la chiBaha’i pochita ntchito kukusokonezeka ndi chisoni pa zotsatira za mliri wu pa mtundu wa anthu. Kalanga! Tikuzindikira kuti okhulupilira ndi abwenzi awo akumvanso kusautsidwa kotere. Kupatukana kwa abwenzi ndi abale kumene, potsatira zofunikira poziteteza, anthu ambiri mu dziko lapansi tsopano akusunga chifuniro, kwa ena, kupereka njira ku kusiyana kwa muyaya. Tsiku lililonse kukuoneka kuti ululu wochuluka uzikhalapo dzuwa lisanalowe. Tipempha lonjezo la kulumikizananso mu ulemelero wosatha kupereka chilimbikitso kwa iwo amene ataya okondedwa awo. Tikupemphera kuti mitima yawo ipepukidwe, ndi chisomo cha Mulungu chizungulire iwo amene maphunziro awo, ntchito, m’makomo awo, ngakhalenso zowalora kupitilira pa moyo zili pa chiopsezo. Kwa inu, ndi iwo amene tikuwanyadira ndi abwenzi onse, tipempha kwa Baha’u’llah ndi kufufuza madalitso ndi chisomo Chake.
Ungatalike ndi kuvuta bwanji mseu umene tiyenera kuyendamo, tili ndi chikhulupiliro chapamwamba pa kulimba mtima ndi kuchilimika kwanu pa ulendo umenewu. Mukutengako kuchokera mu nkhokwe ya chiyembekezo, chikhulupiliro ndi kuganiza kwapamwamba, kuyika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zanu, kulora iwo amene amanidwa chakudya chauzimu, iwo amene ali ndi ludzu lopeza mayankho kuti akhale okhutitsidwa, ndi iwo amene ali ndi khumbo lofuna kutumikira ku ubwino wa dziko lapansi kuti apatsidwe zoyenelera. Kuchokera kwa otsatira odzipereka a Wolungama Wodalitsika, tingayembekeze bwanji zochepa?
Chaka cha kukonzekera ndi kuwunikira, komanso cha kuyesetsa kwakukulu, chafika kumapeto, chopatulika ndi kuyesetsa kwa abwenzi pa dziko lonse kukwaniritsa zaka zana limodzi (100) za kukwera kumwamba kwa ‘Abdu’l-Bahá, kuphatikizapo kutumiza nthumwi kukatenga nawo gawo pa kukumana kwapadera kukumbukira Iye ku Malo Woyera. Kudzera mu kuyesetsa kumeneku, chilimbikitso choperekedwa ndi moyo wa ‘Abdu’l-Bahá chakhudza mizimu yosawerengeka osati ya a Baha’i okha. Kukhudzika kwake pa membala aliyense wa mtundu waanthu, ntchito Yake yophunzitsa, Kutukula kwa ntchito za maphunziro ndi moyo wabwino Kwake, zosonkhera Zake zazikulu ku ntchito zakum’mawa ndi kumadzulo, Chilimbikitso Chake chochokera pansi pamtima pa ntchito zomanga Nyumba Zopembedzeramo, kuthandizira kwake kukhazikitsa zikhazikitso za chiBaha’i za kayendetsedwe, kusonkhanitsa kwake kwa mbali zosiyana-siyana za moyo wa mbumba – zonse izi zoyimira moyo Wake zina Chikumbutso cha kudzipereka kwake kotheratu ndi kopitilira ku kutumikira Mulungu ndi kutumikira mtundu wa anthu. Pamwamba pokhala chiphona cha kutsogolera kwa khalidwe labwino ndi kupambana ziphunzitso zauzimu, ‘Abdu’lBahá anali chodutsiramo changwiro momwe mphamvu yotulutsidwa ndi Chibvumbulutso cha Bahá’u’lláh ingagwilire ntchito pa dziko lapansi. Pofuna kumvetsa mphamvu yomanga dera yomwe ili mu Chipembedzochi, munthu sakufunika kuyang’ananso kwina koma ku zipambano za ‘Abdu’l-Bahá mu nthawi ya utumiki Wake ndi mphamvu zosintha za chitsogozo zomwe zinatuluka mosalekeza kuchokera ku cholembera Chake. Zambiri mwa zipambano zodabwitsa zomwe zikuchitika ndi mbumba ya chiBaha’i yalero – zomwe zinakambidwa m’mauthenga athu kwa inu mu Rizwani yapita – ikukhudza ku chiyambi cha ntchito, ziganizo ndi chitsogozo za
‘Abdu’l-Bahá.
Ndikoyenera bwanji, choncho, kuti chikumbukiro chapamodzi cha mbumba yachiBahá’í kwa Chitsanzo changwiro ichi chikhalenso chiyambi cha kuyambika kwa ntchito yayikulu yolunjika pa kutulutsa kwa mphamvu yomanga dziko ya Chipembedzo pa milingo yayikulu koposa. Mbali za ntchito yomwe ili m’gulu ili la Pulani ya Zaka Zisanu ndi Zinai (9), ndinso mu mndandanda wa Mapulani, zikulunjika ku chikwaniritso cha cholinga ichi chachikulu. Likhalanso thima la misonkhano yoposa 10,000 yomwe ikuchitika padziko lonse lapansi kupanga chiyambi cha ntchito iyi yauzimu yayikulu. Misonkhano iyi, yomwe ikuyembekezera kudzalandira chiwerengero chochuluka cha otenga mbali, ikubweretsa pamodzi osati aBahá’í okha komanso ena ofunira zabwino mtundu wa anthu amene ali ndi chidwi chobweretsa umodzi ndi kupanga dziko kukhala labwino. Kuchilimika kwawo ndi cholinga chawo chachikulu zikuonekera mu uzimu wopezeka mu misonkhano imene yachitika kale, komwe otenga mbali apatsidwa mphamvu kwambiri ndi zokambirana zosiyana-siyana zomwe iwo asonkhera ngati okhala ndi masomphenya apamodzi omwe anawunikidwa ku zochitika zosangalatsa zimenezi. Tikuyang’anira ndi chidwi ku zimene zituluke m’miyezi ndi mzaka zikubwerazi.
Chiperekereni uthenga wathu wapa 30 Disembala 2021 ku msonkhano wa Alangizi, maBungwe Aakulu Auzimu ndi Khonsolo za Mzigawo zachiBaha’i akhala akuwunguza mowona mtima kuthekera kochulukitsa ndondomeko za kukula m’makalasita a m’malire awo mkati mwa Pulani ya Zaka 9. Tikuona kuti zikhala zothandiza, ndicholinga choyesa chitsogolo chomwe chingachitike pakupita kwa nthawi, kuunikanso Pulani pomwe ikutambasuka m’magawo awiri a zaka zinayi (4) ndi zisanu (5), ndipo Mabungwe Aaukulu anafunsidwa kuganizira mtunda umene akuganizira kuwona, mu mbumba zawo pofika Rizwani 2026 kenako Rizwani 2031. Ntchito iyi inakhudzanso kuwunikiranso kwa malire a makalasita, zotsatira za kuwunika kumeneku ndi kwakuti chiwerengero chonse cha makalasita padziko lonse chakwera ndi theka la theka (kota) ndipo tsopano chili pa 22,000. Kutengera malipoti omwe alandiridwa, pali chiyembekezo choti, pofika mapeto a Pulani, pologalamu ya kukula yomwe ili pamtunda wina wake wopita chitsogolo idzapezeka m’makalasita osachepera 14,000 a makalasita onse. Kuchokera mwa amenewa, momwe pologalamu ya kukula idzakhala yafika pa kathithi chiwerengero chitha kuzakwera kufika pa 11,000 mu nthawi yomweyi. Ndipo mwa awa, pali chiyembekezo kuti chiwerengero cha makalasita amene adutsa mtunda wachitatu chidzakwera kudutsa 5,000 pofika 2031. Popanda kukayika, kuti mtunda umenewu udzakwaniritsidwe zikutanthauza kuyesetsa kwakukulu mu Pulani yonse. Koma tikuona kuti awa ndi magolo oyenera kuti tiyesetse kuwafikira, pakuti akuyimira ntchito yayikulu koma yofikirika.
Uku ndi kunena. Zolinga zotere sizikanakhala zoona ndi kuzilingalira pakanakhala kuti zikhazikitso za kayendetsedwe nazo sizinapite patsogolo mowonekeratu, kudzoza izo ndi kuthekera kwakulu kukwaniritsa zochita-chita za mbumba imene ntchito zake zachulukitsidwa mofulumira, kukhudza chiwerengero chopitilira kukula cha mizimu yogwirizana. Sizikanatheka kulakalaka kukula kotere ngati khumbo lofuna kuphunzira – kuchita, kuwunikira, ndi kupeza ziphunzitso, ndi kutenga zophunziridwa zotuluka malo ena – silikanapezeka pa milingo yonse, kufikira kumadera ammidzi ku mbumba. Ndipo kuyesetsa komwe chithuzi-thuzi ichi chikuyimira sikukanakhala kotheka potenga ntchito ya ndondomeko pophunzitsa ndi kusula anthu m’dziko lachiBahá’í. Zonsezi zabweretsa kupita patsogolo kwina kwake mu kuzindikira kwa mbumba yachiBahá’í pa cholinga ndi umunthu wake. Chidwi choyang’ana zinthu zina zozungulira mu ndondomeko yomanga dera chinali chitakhazikitsidwa kale mu zikhalidwe za madera ochuluka; ndipo tsopano yapereka zipatso, mu mbumba zochuluka zomwe zikudzuka, mu udindo weni-weni pa kupita patsogolo muuzimu ndi kuthupi kwa magulu akulu-akulu a anthu a m’madera, kufikira anthu ena osakhala aBahá’í. Kuyesetsa kwa abwenzi kamanga mbumba, kutenga mbali pa ntchito ya chitukuko cha m’madera, ndi kusonkhera ku ntchito zosiyana-siyana za’mdera zakhala ntchito imodzi yadziko lonse, yomangidwa pamodzi ndi ndondomeko yapamodzi yogwilira ntchito, yolunjika pa kuthandiza mtundu wa anthu kukhadzikitsa zinthu zake pa maziko a mfundo zauzimu. Kupatulika kwa zitukuko zomwe tafotokoza, kufikira apa zaka 100 chikhadzikitsireni Ndondomeko ya Kayendetsedwe, sikungayiwalidwe. Mu kukwera kodabwitsa kwa kuthekera kumene kwaoneka m’zaka nakumi awiri zapitazo – ndipo zomwe zapangitsa kuthekera kuti dziko lachiBahá’í liwunikira ntchito zake potengera mphamvu zotulutsidwa zomanga madera za Chipembedzo –tikuona umboni wokwanira kuti Chipembedzo cha Mulungu chalowa mu ndime yachisanu ndi chimodzi ya Kumanga (Formative Age). Tinalengeza mu Rizwani yapita kuti kufalikira kodabwitsa pa kutenga mbali kwa chiwerengero chochuluka mu zochitika-chitika zachiBahá’í, koyatsidwa ndi chikhulupiliro, ndi kupeza maluso ndi kuthekera koti atumikire madera awo kunaonetsa kuti gawo lachitatu la Pulani Yoyera ya Abdu’l-Baha inayamba; Pulani Ya Chaka Chimodzi, poyambilira pake kenako tsopano kumapeto, yayambitsa mbiri ya kutukuka komwe kwachitika ndi gulu la okhulupilira. Ndipo pachiyambi cha ntchito yatsopano yayikulu, thupi ili logwirizana la okhulupilira layima mokonzeka kutenga mwayi omwe watsegulidwa kwa ilo.
Chizindikiro chowonekeratu cha gawo lomwe tsopano likufika pamapeto linali kumanga kwa Nyumba Yopembedzera yomaliza ndi kuyambika kwa mapolojekiti wokhazikitsa Nyumba Zopembedzera m’maiko komanso m’zigawo za m’maiko. Zambiri zaphunziridwa, ndi aBaha’i padziko lonse, zokhudza Nyumba Zikuluzikulu Zopemphereramo (Mashriqu’l-Adhkár) ndi mgwirizano wa kupembedza ndi kutumikira komwe imayimira. Mkati mwa gawo la chisanu ndi chimodzi (6) la Ndime Yomanga, zambiri ziphunziridwa zanjira yomwe ikuchokera mu chitukuko cha mkati mwa mbumba ya moyo wapemphero wabwino – ndi kutumikira komwe imalimbikitsa – kufikira pa kuonekera kwa Nyumba Zikuluzikulu Zopemphereramo. Zokambirana zikuyambika ndi maBungwe Aakulu Auzimu, ndipo pomwe kukupitilira, tizilengeza pafupi-pafupi malo kumene Nyumba Yopembedzera yachiBaha’i yamangidwa mu zaka zikubwerazi.
Chimwemwe chathu powona mbumba ya Dzina Lalikulu ikulimbitsidwa chikumasokonezeka ndi chisoni chathu chachikulu powona kupitilira kwa mavuto ndi kulimbana padziko zomwe zikumabweretsa chisoni ndi kuvutika kwakulu – maka, powona kubadwanso kwa mphamvu zowononga zimene zasokoneza maubale a maiko pomwenso zoopsa zazikulu zikuchitikira makamu a anthu. Tikudziwa bwino lomwe ndipo tili wotsimikiziridwa kuti, ngati mbumba zachiBahá’í zaonetsa mobwereza-bwereza munjira zosiyana-siyana, otsatira a Bahá’u’lláh ndi odzipereka pa ntchito yochepetsa kuzunzika ndi kuthandiza iwo amene awazungulira, posatengera momwe iwo eni alili. Koma pokha-pokha mtundu wa anthu onse uchilimika kukhazikitsa ntchito zake pa maziko a chilungamo ndi choona, izi, Kalanga, zitha kubweretsa masautso opitilira. Tikupemphera kuti, ngati kuyambika kwa nkhondo posachedwapa kumaiko a azungu (Europe) kungabweretse maphunziro alionse pazatsogolo, idzatumikira ngati Chikumbutso pa mbali imene dziko liyenera kutenga ngati likufuna kupeza mtendere weni-weni ndi wopitilira. Mfundo zimene zinanenedwa ndi Baha’u’llah ku mafumu ndi mapulezidenti a nthawi Yake, ndi maudindo aakulu amene Iye anapereka kwa olamulira kalelo ndi panopa, tsopano utha kuoneka kufunika kwake lero kusiyana ndipo unalembedwa poyamba ndi Cholembera Chake. Kwa aBahá’í, kupita patsogolo mosakayika kwa Pulani Yayikulu ya Mulungu – kubwera pamodzi ndi mayesero ndi zosokoneza, koma mapeto ake kumema mtundu wa anthu ku chilungamo, mtendere, ndi mgwirizano – ndimomwe Pulani Yaying’ono ya Mulungu, imene okhulupilira atangwanika nayo kwakukulu, ikutambasukira. Kusalongosoka kwa zinthu m’tsiku lalero kukupangitsa kufunika kotulutsa mphamvu yomanga dera ya Chipembedzo kumveka mokwanira ndi motsindika.
Sitingayembekezere zina, pakali pano, koma kupitilira kwa kusokonezeka ndi kutekeseka kwa dziko; inu mosakayika muyamikira, choncho, kuti mpofunika kuti kupemphera koona mtima kulikonse komwe tikupereka kwa ana onse a Mulungu kuti amasulidwe mu mazunzo owawa ndikophatikizanso ndi pemphero la pansi pamtima pa kupita patsogolo kwa kutumikira komwe kukufunika panopa komwe mukupereka ku Chipembedzo cha Kalonga wa Mtendere.
Mu kalasita ina iliyonse zochita-chita za Pulani zayamba kupita patsogolo, tikuona kutukuka kwa mbumba ndi makhalidwe otamandika omwe tinafotokoza mu uthenga wamu 30 Disembala 2021. pomwe madera akukumana ndi mavuto a mitundu yosiyana-siyana, otsatira a Wokongola Wakumwamba ayenera kusiyana ndi ena pa makhalidwe awo a kupilira ndi nzeru, pa machitidwe awo ndi kutsatira mfundo, ndi kukhala a chifundo, odzipatula, ndi kulolerana komwe akuonetsa pofuna-funa mgwirizano. Nthawi ndi nthawi, makhalidwe opatulika ndi mchitidwe omwe okhulupilira akuonetsa mu nyengo zovuta kwambirizi zapangitsa anthu kutembenukira kwa aBaha’i pofuna chifotokozo, malangizo, ndi thandizo, maka pomwe moyo wa dera wasokonezeka ndi zosokoneza zosakonzekera. Pogawana izi, tikukumbukira kuti mbumba yachiBahá’í payokha nayonso ikukumana ndi zotsatira za mphamvu zowononga zimenezi zomwe zikugwira ntchito padziko lonse. Kuonjezera apo, tikuzindikira kuti kukula kwa kuyesetsa kwa abwenzi potukura Liu la Mulungu kupitilira, ndipomwenso akumane ndi mphamvu zolepheretsa, posakhalitsa kapena mtsogolo, kuchokera mbali zosiyana-siyana. Iwo ayenera kulimbitsa maganizo ndi mizimu yawo ku mayesero omwe abwera ndithu, kuti izi zisakhale zobwezeretsa m’mbuyo ntchito zawo. Koma okhulupilira akudziwa bwino lomwe kuti zovuta zina zilizonse zomwe zili mtsogolo mwawo, bwato la Chipembedzo ndilofana ndi iwo onse. Ndime zotsatana za ulendo wake zakumana ndi nyengo zimenezi ndipo zadutsa mafunde ake. Tsopano zikulunjika panjira yatsopano. Zitsimikizo za Wamphamvu Yonse ndi mweya umene ukuzaza paulendo wake ndikuyingolera iyo ku mapeto aulendo wake. Ndipo Pangano ndi nyenyezi yachitsogozo, kuonesetsa kuti bwato lili panjira yake yeni-yeni. Tipempha ochezera alendo akumwamba atumize madalitso awo pa onse omwe ali paulendo umenewu.
Tikukulonjerani mu kuwala kwa nyengo zosayiwalika zomwe zimapanga chikondwelero cha zaka 200 za kubadwa kwa Wokongola Wodalitsikayo. Pomwe tikuganizira zomwe zinachitika nthawi iyi komanso kuyambira pamenepa, tikupeza kuti mbumba yachiBaha'i ya dziko lonse yapano silinso chimodzi-modzi ndi pomwe imayamba paulendo wake ma sayiko asanu ndi imodzi a Pulani yapanoyi. Ili yokhudzika kuposa mmbuyomu ndi ntchito yake. Yaonetsa kuvumbulutsika kwakulu pa kuthekera kwake kubweretsa abwenzi ndi ogwira nawo ntchito limodzi mu mngwirizano ndi moyo wa mbumba; kutsogolera madera ndi midzi mu ntchito yogwirizana; kukambirana momwe zoonadi zauzimu zingamasulilidwe mu ntchito yopitilira; komanso, kupitilira apo; kukambirana osati za ziphunzitso zomwe zingamange dziko latsopano kokha, komanso zokhudza Iye Amene adaphunzitsa izo: Baha’u’llah. Nkhani za moyo Wake ndi kuzunzidwa Kwake zokambidwa ndi malilime ochuluka a akulu, achinyamata ndinso ana zinakhudza mitima yosawerengeka. Ena anadziwonetsa okha kuti akonzeka kufufuza Chipembedzo Chake mopitilira. Ena analonjeza kutenga nawo mbali. Ndipo mizimu yambiri yomasuka inasunthidwa kutsimikizira ku chikhulupiliro chawo.
Chimodzi mwa zoonetsa zonenedwa za kupita patsogolo kunali malo ochuluka komwe kunaonekeratu kuti Chipembedzo chadzuka kuchokera ku kusadziwika mu mdziko. Panali atsogoleri a boma and atsogoleri ena amene ananena poyera – ndiponso nthawi zina kutsindika mwapadera- kuti dziko likufunika masomphenya a Baha’u’llah ndipo kuti ntchito za aBaha’i ndi zosililika ndipo zikuzidwe. Chinatikondweretsa ife kuona kuti si aBaha’i okha amene anafuna kulemekeza Baha’u’llah ndi kukondwelera moyo Wake – kusonkhana kwapadera kunachitika ndi ena osakhala aBaha’i. M’madera momwe muli kusagwirizana ndi Chipembedzo, abwenzi sanaope, iwo anaonetsa kumasuka kodabwitsa, analimbikitsa amnzawo kufufuza choonadi mwa iwo okha, ndipo ambiri anatenga nawo mbali pa zikondwelero mosangalala. Chikondwelera cha zaka 200 zakubadwa kwa Baha'u'llah kunapangitsa kudzuka kwa maluso osiyana-siyana a zisangalaro, umboni waukulu wa kasupe wa chikondi momwe unachokera. Khalidwe la mbumba yachiBaha’i ku kapangidwe ka chikondwelero ichi linali momwe zambiri zaphunziridwira kwa zaka zoposa makumi awiri tsopano, chiyambireni mndandanda wapano wa mapulani a zaka zisanu. Wokhulupilira payekha anatengapo mbali, mbumba inadzuka kugwira ntchito limodzi, ndipo abwenzi analunjikitsa mphamvu zawo ku mapulani okonzedwa ndi zikhadzikitso. Chikondwelero chopatulika, kukwaniritsa kudutsa kwa zaka zikwi ziwiri, zopereka kudzuka kwa mphamvu kwambiri ku ntchito yomanga mbumba ku zaka zina chikwi zili mkubwera. Munyengo yotsogozana ndi chikondwelero china cha zaka 200 chachiwiri, lolani mbeu iliyonse yodzalidwa ndi chikondi pa chikondwelero choyamba ileledwe modekha kuti ipereke zipatso.
Zaka ziwiri mu Pulani yapano, ngakhale kuti kupita patsogolo mosakakamiza sikungakhale kofanana mdziko lililonse, chiwerengero cha mapologalamu a kukula a kathithi padziko lonse chikuyandikira theka la nambala ya 5000 yomwe inayikizidwa mu ntchito za pulani yapanoyi, ndipo mlingo umene nambalayi ikukwelera wakhala ukukula. Kuyang’anitsitsa mchifupi, pali zizindikiro zolonjeza za momwe mphamvu ndi kuthekera kwa anthu, mbumba ndi zikhadzikitso zikuonekera. Kwa okhulupilira kulikonse, kuphunzira kwa zaka 200 za chikondwelero komwe kunaonetsera kuti kukambirana kwawo kwa tsiku ndi tsiku ndi anthu owazungulira kukhoza kulumikizitsidwa ndiuzimu wa kuphunzitsa. Ndipo pomwe ntchito mmidzi mazana-mazana ndi mmadera ikupita patsogolo, moyo wokhadzikika wa mbumba ukukhadzikika monsemo. Chiwerengero cha makalasita komwe ndondomeko yokulitsa patani ya zochita ku madera ochuluka ikukhadzikika bwino lomwe – kulora, chomwecho, abwenzi kudutsa mtunda wachitatu pa mndandanda wa kukula chapita patsogolo kwambiri. Ndi apa, pamalo ophunzirira aBaha’i padziko lonse, makamaka poyendetsa miyanda-miyanda ya anthu ku masomphenya a Baha'u'llah, kumene osati chiwerengero chachikulu chikubwera kutenga nawo mbali mu zochita-chita za aBaha’i komanso abwenzi tsopano akuphunzira momwe magulu ang’ono-angóno akuzizindikiritsa okha ndi mbumba ya Dzina Lalikulu Kwambiri. Tikuona kuyesetsa pa maphunziro a Chipembedzo akuyamba kutenga chikhazikiko chabwino mmalo amenewa, pomwe ana akuyenda mosajejema mu mndandanda wa maphunziro chaka ndi chaka komanso mlingo umodzi wa maphunziro auzimu a achinyamata achisodzera ukusuntha kufika pa mlingo wina. Mmalo amenewa, insitichuti zikuphunzira kuonesetsa kuti anthu okwanira otumikira akusulidwa kuti athe kupereka maphunziro auzimu ndi chikhalidwe cha ana ndi achinyamata achisodzera omwe chiwerengero chawo chikukulira-kulira. Kutenga mbali mu zochita-chita izi zomanga maziko mwa ana kukuyamba kukhadzikika mzikhalidwe za unyinji omwe umaonedwa monga mbali imodzi yofunika ya moyo wa mbumba. Nyonga zatsopano zikuyamba kutuluka mwa anthu omwe akutenga chitsogolo cha chitukuko chawo chomwe, ndipo akumanga chitetezo ku mphamvu zam’dera zomwe zimabweretsa maganizo osemphana. Kuthekera kwa kupita patsogolo kwa kuthupi ndikuuzimu kukuoneka. Uweniweni wadera wayamba kusintha.
Abwenzi okondedwa, iyi ndithudi ndi nthawi yopereka mathokozo kwa Wokondedwa Wabwino. Pali zifukwa zambiri zazikulu zolimbikitsa. Komabe tikuzindikira bwino lomwe za kukula kwa ntchito yomwe yatsalira. Chofunikira, momwe tidanenera mmbuyomu, kuyenera kuonekera mma kalasita ochuluka gulu lopitilira la okhulupilira amene angathe, ndi ena owazungulira, kupitiliza ntchito yokulitsa ndi kumanga kuthekera, ndi amene angasiyanitsidwe kamba ka kuthekera kwawo ndi khalidwe kuunikira pa ntchito ndi kuphunzira kudzera mu kuchita. Kukulitsa ndi kuyendera limodzi ndi gulu la anthu mmalo aliwonse – osati mkalasita mokha komanso mmadera ndi mmidzi – ndi ntchito yovuta koma yofunika kwambiri. Koma komwe izi zikuchitika, zotsatira zikuchitira umboni.
Ndife achikhulupiliro kuona kuti zikhadzikitso za Chipembedzo zikusunga kufunika uku kwakukulu patsogolo pa maganizo awo, kupeza njira zabwino zothandizira kuphunzira kochokera mu kupita patsogolo kuti kugwire ntchito mmadera ambiri. Panthawi yomweyo, kuphunzira kwakukulu kukupereka ku zikhadzikitso za mdziko, mzigawo,ndi mmadera masomphenya aakulu. Zayamba kukhudzidwa m’mbali zonse za chitukuko cha mbumba ndipo ndi okhudzidwa ndi ubwino wa anthu osati mamembala ake okha. Pozindikira zovuta zokhadzikika zomwe ndondomeko ya insitichuti ili nazo pa kutukuka kwa anthu, zikupereka chidwi chachikulu pa momwe ma insitichuti angalimbitsidwe. Zikukhala okhudzika pa kufunika kolimbitsa chidwi cha mbumba pa zofunika za Pulani ndi kuyitanira gulu la abwenzi lokulira-kulira ku milingo yayitali ya umodzi. Zikukweza mokhulupirika udindo wawo kukonza bwino ndondomeko zawo za kayendetsedwe ndi zachuma kuti ntchito ya kukula ndi kulimbitsa ithandizidwe bwino. Mu zonse izi, zikukhala zotanganidwa ndi kupeza mu mbumba zoyenelera zomwe zingapangitse kutulutsa mphamvu zauzimu.
Pomwe ntchito ya kumanga mbumba ikukula, abwenzi akugwiritsa ntchito kuthekera kwatsopano komwe apeza kusintha kakhalidwe ka mdera lowazungulira, mphamvu zawo zayasidwa kamba ka kuphunzira kwa ziphunzitso zoyera. Ntchito za kanthawi pang’ono nazonso zakwera mchiwerengero, ntchito za ndondomeko nazo zakulanso, ndipo tsopano kuli zitukuko zochuluka zachiBaha’i zomwe zikugwira ntchito ya maphunziro, umoyo, zaulimi ndi mbali zina. Kuchokera mu zotsatira za kusinthika zoonekeratu mwa munthu komanso mmiyoyo pamodzi ya anthu ikusiyanitsa zoyambitsa zosasokonekera za mphamvu yomanga dera ya Chipembedzo cha Baha’u’llah. Nchifukwa chake, tsono, kuchokera mu zochitika izi za ntchito za mdera – zophweka kapena zolimba, za nthawi yayifupi kapena yayitali – maofesi oona za Mbumba yachiBaha’i ya Kunja (Baha’i International Community) akupeza chilimbikitso mopitilira mu kuthekera kwawo kutenga mbali mu ntchito zosiyana-siyana za dera. Iyi ndi mbali imodzi ya ntchito ya Chipembedzo imene yachita bwino. Pa mlingo wa dziko, zosonkhera ku ntchito zomwe zili za tanthauzo mdera – kufanana kwa amuna ndi akazi, maulendo ndi kuchitira limodzi, udindo wa achinyamata pa kusinthika kwa ntchito za chitukuko, ndi kulolerana kwa Zipembedzo, kungotchulapo zina – zikupangidwa ndi kudzikhulupilira kwakukulu, luso, ndi kuzindikira. Ndipo kulikonse komwe akukhala, kugwira ntchito, kapena kuphunzira, okhulupilira a misinkhu yonse ndi mitundu yonse akusonkhera kwakukulu ku ntchito zina zofunikira, kubweretsa kuzindikira kwa iwo amene awazungulira iwo njira yabwino yowumbidwa ndi Chibvumbulutso chachikulu cha Baha'u'llah.
Kukhadzikika kwa Chipembedzo mmalo osiyana-siyana momwe ntchito ikutambasuka kwakhala kukupita patsogolo ndi kupezeka kwake pa makina a intaneti a dziko lonse, kupezeka komwe kwakula kwambiri kudzera mu kukhadzikitsa kwama webusayiti ochuluka achiBaha’i ndi kukuza kwa masayiti ena pa Baha'i.org. Izi zili ndi ubwino waukulu ku ntchito ya kufalitsa ndi kuteteza Chipembedzo. Kwa masiku ochepa okha gulu la anthu lochuluka linakopeka ku zolemba zosamala bwino zokhudza Chipembedzo zomwe zinayikidwa pa webusayiti ya chikondwelero cha zaka 200 zomwe zinayikidwa mzinenero zisanu ndi zinai, ndipo tsopano zakuzidwa mmaiko paokha-paokha kufotokoza kusakanikirana kwa zikondwelero zomwe zinachitika. Mapulani ali kale mkati kuti kukhadzikitsidwe webusayiti yosungirako uthenga (Reference Library) yachiBaha’i, chipangizo chimene chipereke mwayi ku ma Tabuleti osamasulilidwa ndi kusindikizidwa a mMalembo Oyera kuti atulutsidwe pamenepo. Pamwamba pa izi, mabuku a Zolemba za Baha'ú'llah ndi Abdu’l-Baha zomwe zayikidwa mchingerezi tsopano zioneka mzaka zikubwerazi.
Ku Santiago, Chile ndi Battambang, Cambodia, Nyumba Zopembedzeramo zatsopano padziko lonse zikuyamba kukhala malo achikoka, zizindikiro za chimene Chipembedzo chikuyimira. Ndipo chiwerengero chawo chikula posachedwa. Ndife okondwa kulengeza kuti mwambo woyikiza Nyumba Yopembedzera yaku Colombia, Norte del Cauca, udzachitika mwezi wa Julaye. Kupitiliza apo, kumanga kwa Nyumba Zopembedzera zoonjezera kuli chifupi. Ku Vanuatu, ntchito yotenga chilolezo ili mkati kuti Nyumbayi iyambe kumangidwa. Ku India ndinso ku DR Congo, ndondomeko yayikulu ndi yokhwima tsopano yamalizidwa yomwe yathandiza kupeza malo oti padzamangidwe Nyumbazi. Chisangalaro poona ndondomeko ya kamangidwe ka Mashiriku-Adhkar yoyamba ku Papua New Guinea pa Naw-ruz kunafika pamodzi ndi kuwulutsa ndondomeko ya momwe Nyumba Yopembedzera yamdera idzamangidwire ku Kenya. Pakadali pano, tili ndi chiyembekezo kuti mauthenga omwe anatulutsidwa posachedwa okhudza chikhadzikitso cha Mashriku-Adhkar, okonzedwa ndi Nthambi yathu ya Kafukufuku, apitiliza kupanga abwenzi kuyamikira kufunika kwa kupembedza pa moyo wa mbumba. Pakuti mu ntchito zawo zakutumikira, makamaka, mmisonkhano yawo ya mapemphero, aBaha'í kulikonse akuyika maziko auzimu a Nyumba Zopembedzera za mtsogolo.
Tsopano kwatsala zaka zitatu zokha za ntchito ya kota ya zaka theka la chikwi yomwe inayamba mchaka cha 1996 yomwe imalunjika kwambiri pa golo limodzi: kupititsa patsogolo kulowa mwaunyinji. Pa Rizwani 2021, otsatira a Baha'ú'llah adzayamba Pulani ya chaka chimodzi. Yayifupi, koma yodzadza ndi chenjezo, ntchito iyi ya chaka chimodzi idzayambitsa funde latsopano la Mapulani onyamula chombo cha Chipembedzo kupita ku zaka 100 za ndime yachitatu yachi Baha'í. Mu miyezi imeneyi khumi ndi iwiri, kukumbukira kwa dziko lachi Baha'í kwa zaka 200 za kukwera kumwamba kwa Abdu’l-Baha kuzaphatikizapo mwa zina msonkhano ku Likulu la aBaha'í komwe oyimira a Mabungwe Auzimu a Mmaiko ndi makhonsolo onse adzayitanidwa. Ichi, komabe, chidzakhala chinthu choyambilira mu mndandanda wa zochitika zomwe zidzakonzekeretsa okhulupilira ku ntchito ya zaka za mtsogolo. M’mwezi wa januwale chaka chotsatira, kukwaniritsa zaka 100 chiwerengereni poyera Chifuniro cha Abdu’l-Baha idzakhala nthawi ya msonkhano waukulu ku Malo Oyera kubweretsa pamodzi Alangizi ndi Athandizi awo a kuteteza ndi kufalitsa. Mphamvu zauzimu zomwe zidzatulutsidwe ku misonkhano imeneyi mu mbiri ya Chipembedzo zidzayenera kufikira kwa abwenzi onse a Mulungu ku mbali iliyonse ya dziko yomwe akukhala. Pa chifukwa ichi, mndandanda wa misonkhano udzachitika mmiyezi yotsatira, yotsogolera ku ntchito ya zaka zochuluka zomwe zidzatsatira pamapeto pa Pulani ya Chaka Chimodzi.
Ndime yatsopano ya kutambasuka kwa Pulani Yoyera ya Abdu’l-Baha ikubwera. Koma masomphenya osangalatsa ndi a posachedwa ali patsogolo pathu. Chikondwelero cha zaka 200 za kubadwa kwa Bab chili pafupi, chaka ndi theka zikubwerazi. Iyi ndi nyengo yokumbukira kudzipereka molimba mtima kwa Martyr-Herald (Mkupamame wa a Maritiri) wa Chipembedzo chathu, Yemwe ntchito yake yodzadza ndi zotchinga inakankhira mtundu wa anthu ku ndime yatsopano ya mbiri. Ngakhale ikusiyanitsidwa ndi zaka pafupi zikwi ziwiri ndi nthawi yathu ino, mbumba yomwe Bab anaonekera ikufanana ndi dziko la lero chifukwa cha kuponderezana ndi kufunitsitsa kwa anthu ochuluka kupeza mayankho okwaniritsa ludzu la mzimu lofuna kudziwa. Poganizira za momwe zisangalaro za zaka 200 izi zidzakhalire, tikuzindikira kuti zikondwelero zimene zidzakhala zapadera-dera. Komabe, tikuyembekezera zochita-chita zosachepera zochuluka ndi zozadza monga momwe zinalili pa zikondwelero 200 zapita. Ndi mwambo umene mbumba iliyonse, nyumba iliyonse, mtima uliwonse mosakayika udzayangánirako ndi chiyembekezo.
Miyezi iwiri yotsatira idzakhalanso nthawi yokumbukira miyoyo ya omtsatira a Bab olimba mtima – (heroes and heroines) amene chikhulupiliro chawo chinaonetsedwa mu ntchito za kudzikhuthula kosafanizirika kumene kudzakongoletsa mbiri ya Chipembedzo. Makhalidwe awo opanda mantha, kudzipereka, ndi kudzipatula ku zilizonse koma Mulungu kukhudza iwo okha pa aliyense amene adamva za ntchito zawo. Ndi zokhudza bwanji, indedi, msinkhu wawo wachichepere pomwe ambiri olimba mtimawa anasiya chizindikiro chosayiwalika ku mbiri. Mu nthawi ikubwerayi, chitsanzo chawo chipereke kulimba mtima ku gulu lonse la okhulupilira – maka achinyamata, amene akuyitanidwanso kutsogolera ntchito yomwe cholinga chake ndi kusintha dziko lapansi.
Ichi, tsono, ndi chikhulupiliro chathu chowalitsitsa. Mu masayiko asanu ndi imodzi amene ali mu Rizwani yapano kufikira chikondwelero cha zaka 200 za Bab zikubwerazi – indedi, mu zaka zitatu zotsalazi pofika mapeto a Pulani ino – lolani chikondi chomwecho chomiza ndi chopatulika chomwe chinalimbikitsa omsatira a Bab kugawa kuwala koyera kukulimbikitseni inu ku ntchito zazikulu. Kuti inu mukhale zolandiriramo za thandizo la kumwamba, ndi pemphero lathu ku Malo Oyera.
Pomwe Chikondwelero Chachikulu Kwambiri chayandikira, tadzazidwa ndi mathokozo ndi chiyembekezo—kuthokoza pa zodabwitsa zimene Bahá’u’lláh wathandizira omutsatira Ake kukwanilitsa, chiyembekezo pa zomwe zili mtsogolo.
Mphamvu zomwe zinapezeka pa chikondwelero cha dziko lonse cha zaka 200 za kubadwa kwa Bahá’u’lláh zangopitilira kukula. Kupita patsogolo mofulumira kwa mbumba yachiBaha’i, kukwera kwa kuthekera kwake, ndi kutha kutapa mphamvu kuchokera mwa ambiri a mamembala ake kukuonekeratu kuchokera muzikwanilitso zaposachedwapa za dziko lonse. Mwa izi, kuchuluka kwa zochita-chita zomanga mbumba makamaka ndi zimene zaonekera kwambiri. Pulani za Zaka Zisanu yapano ikutsatira zaka makumi awiri za kuyesetsa kwa dziko lachiBaha’i kukonza ndi kuchulukitsa zochitikazi mwadongosolo— koma choyamikika, mu zaka ziwiri ndi theka za Pulaniyi, chiwerengero cha zochitikachitika pazokha chakwera kudutsa theka. Mbumba ya dziko lonse yaonetsa kuthekera kobweretsa anthu, nthawi ina iliyonse opitilira miliyoni mu zochita-chita zotere, kuwathandiza iwo kufufuza ndi kuvomera ku zoonadi zauzimu. Mu nyengo yayifupi yomweyi, misonkhano ya mapemphero nayo yawonjezereka pafupi-fupi kawili-yankho lofunikira kwambiri ku chibalaliko cha mtundu wa anthu chimene chikukulira-kulira ku Kasupe wa chiyembekezo ndi madalitso. Kupita patsogolo uku kwatenga lonjezo lapadera, pakuti misonkhano ya mapemphero imabweretsa mzimu watsopano mu moyo wa mbumba. Molukana ndi kuyesetsa kwa maphunziro a anthu onse, imalimbitsa cholinga chauzimu cha kuyesetsa kumeneku: kukulitsa mbumba zodziwika ndi chikondi chawo cha Mulungu ndi kutumikira kwawo ku mtundu wa anthu. Kulibenso kwina koma izi zaonekeratu koposa mma kalasita amenewa momwe kutenga mbali kwa chiwerengero chochuluka mu zochita-chita zachi Bahá’í zikupitilira mosalekeza ndipo abwenzi adutsa mtunda wachitatu pa kupita patsogolo kwa mbumba zawo. Ndife okondwa kuona kuti chiwerengero cha makalasita komwe ndondomeko ya kukula yapita patsogolo kufika apa yachulukanso kuposera theka chiyambireni cha Pulani ndipo pano chiwerengero chafika pa 500.
Kafuku-fuku uyu wachidule sangapereke chithuzi cheni cheni ku makulidwe a kusinthika komwe kukuchitika. Maonekedwe a zaka ziwiri zomwe zatsala za Pulani ndi owala. Zambiri zakwanilitsidwa mu chaka chathachi popereka maphunziro mokwanira ophunzilidwa kuchokera ku mapologalamu amphamvu a kukula mma kalasita amene monga timayembekezera, kuti akhale nkhokwe za kuphunzilira ndi zipangizo.Sentala Yayikulu ya Kuphunzitsa (ITC), ma khansala, ndi owathandizira awo sanalekeze poonesetsa kuti abwenzi m’mbali zonse za dziko atha kupindula kuchokera kufulumiza pa kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito zophunziridwa zomwe zikupezeka mu makalasita awo. Tili osangalala kuona kuti mma kalasita ochuluka, komanso m’madera ndi m’midzi owazungulira, gulu la abwenzi latuluka amene kudzera mu ntchito zawo ndi kauni-uni akupeza zomwe zikufunikira, kuti ndondomeko ya kukula ipitilire patsogolo mmadera owazungulira. Akugwiritsa ntchito chida chothekera cha maphunziro a insitichuti, momwe kuthekera kosonkhera ku chitukuko chauzimu ndi kuthupi kwa mbumba kukupita patsogolo, ndipo pomwe akugwira ntchito, chiwerengero cha iwo amene akuwatsatira chikukula. Ndi chachidziwikire, madera ndi osiyana-siyana, ngakhalenso makulidwe. Koma kudzera mu kuyesetsa kwa dongosolo, aliyense akhoza kusonkhera mochilimika ku ntchito yomwe ilipo. Pamalo alionse, pali chisangalaro changwiro pochita kukambirana kwa tanthauzo ndi kolimbikitsa ndi mizimu ina, komwe kumabweretsa, mwachangu kapena mwapang’ono-pang’ono, kusunthika muuzimu. Pamene kuwala kwa lawi lomwe layatsidwa mumtima mwa wokhulupilira kuwalira-walira, mphamvu ya chikoka mwa iwo amene akhuzidwa ndi kutentha kwake nayonso imakula. Ndipo kwa mtima umene wamizidwa ndi chikondi cha Bahá’u’lláh, ndi chitinso chinthu china chofunikira koposa kufuna-funa mizimu yofanana nayo, kuwalimbikitsa pamene akulowa panjira ya kutumikira, kuyendera nawo limodzi pomwe akuphunzira ndi-mwinanso chisangalaro chachikulu pa zonse- kuona mizimu itatsimikizika mu chikhulupiliro chawo, kudzuka payokha, ndikuthandiza ena pa ulendo womwewu. Izi ndi zina mwa nyengo zapamwamba kwambiri zomwe moyo uwu waufupi ungakwaniritse.
Masomphenya opititsa patsogolo ntchito iyi yauzimu apangidwa osangalatsa ndi kuyandikira kwa chikondwelero cha zaka 200 za kubadwa kwa Báb. Monga chikondwelero chomwe chinapita, ichi ndi chikondwelero chopambana kwambiri. Chikupereka kwa aBahá’í onse Mwayi waukulu wodzutsa iwo amene awazungulira ku Tsiku la Mulungu lalikulu, ku kusefukira kodabwitsa kwa chisomo cha kumwamba kovumbulutsidwa ndi kuonekera kwa Abvumbulutsi awiri Oyera, Nyenyezi zotsatana Zomwe zinawalitsa dziko lonse lapansi. Muyeso wa zimene zikhoza kutheka mu ma sayiko awiri akubwerawa ndi wodziwika kwa onse kuchokera mu kuphunzira kochokera ku chikondwelero za zaka 200 za kubadwa kwa Baha’u’llah chomwe chinachitika zaka ziwiri zapitazo, ndipo zonse zimene zidaphunziridwa panthawi imene ija ziyenera zigwiritsidwe ntchito pa mapulani a zikondwelero za Aneneri Oyera Amapasa chaka chino. Pomwe chikondwelero cha zaka 200 za kubadwa kwa Bab kukuyandikira, tipemphera mosalekeza mmalo mwanu ku Manda Oyera, kupemphera kuti kuyesetsa kwanu kudzapereka ulemu waukulu kwa Bab kudzapambane kupititsa patsogolo Chipembedzo chomwe Iye analosera.
Kutsekera kwa zaka 100 za Nyengo Yomanga kwangotsalira zaka ziwiri ndi theka. Kudzakwanilitsa zaka 100 za kuyesetsa koyera kulimbitsa ndi kukulitsa maziko amene anayikidwa modzikhuthula mu Nyengo ya Kulimbatima ya Chipembedzo (Faith’s Heroic Age). Pa nthawi yomweyi mbumba yachiBaha’i idzakumbukiranso zaka 100 za kukwera kumwamba kwa ‘Abdu’l-Bahá, nthawi imene Mbuye wokondedwa anamasulidwa mu dziko ili ndi kukakhalanso ndi Bambo Ake mu ulemelero wosatha. Maliro Ake, amene anachitika tsiku lotsatira, anali chochitika “chimene Palesitina anali asanachioneko” Ku mapeto kwake, thupi Lake linayikidwa mu chipinda cha Manda a Bab. Komabe, kunaloseredwa ndi Shoghi Effendi kuti umu ndimongoyembekezera. Manda oyenera chikhalidwe ndi udindo wapamwamba wa Abdu’l-Baha adzayenera kumangidwa nyengo yoyenera ikadzafika.
Nthawi imeneyi yafika. Dziko lachiBaha’i likumemedwa kumanga nyumba imene idzasunga thupi loyeralo mpaka muyaya. Nyumba imeneyi imangidwe mkati mwa munda wa Rizwani, pamalo omwe mapazi a Wokongola Wodalitsika anayeretsapo; Manda a Abd’ul-Baha adzakhala pakati pa Manda Woyera ku Akka ndi Haifa. Ntchito yopanga chifani-fani cha nyumbayi ili mkati, ndipo zambiri zidziwika mmiyezi ikubwerayi. Chimwemwe chosaneneka chikusefukira mkati mwathu, pomwe tikuganizira za chaka chikubwerachi ndi zonse zimene chikulonjeza. Tikuyang’anira kwa wina aliyense wa inuiwo amene ali pa kaliki-liki kutumikira Bahá’u’lláh, kugwira ntchito mu dziko lililonse yobweretsa mtendere-kukwanilitsa kuyitanidwa kwanu kwapamwamba.
1. Mawu omaliza mu ndime yosayiwalika mu mbiri ya Chipembedzo tsopano alembedwa, ndipo tsamba latsegulidwa. Rizwani iyi ikukwaniritsa kumalizitsa kwa chaka chamtengo wapatali, cha Pulani ya Zaka Zisanu, ndi mndandanda wonse wa Pulani omwe unayamba mu chaka cha 1996. Mndandanda watsopano wa Mapulani ukukodola, ndi miyezi khumi ndi iwiri yomwe itumikire ngati mkupamame wa Pulani ya Zaka Zisanu ndi Zinayi (9) yomwe iyambe Rizwani yotsatira. Tikuona patsogolo pathu mbumba yomwe yapeza mphamvu mofulumira ndipo ndi yokonzeka kupita patsogolo. Koma pasakhale kunamizana pa momwe kuyesetsa kwakulu kunafunikira kuti tifike pamenepa ndi momwe zophunziridwa zinapezekera movutikira mkati mwa ndime: maphunziro omwe apezeka adzaumba tsogolo la mbumba, ndipo nkhani zamomwe adaphunzilira kukupereka chithuzi-thuzi cha zomwe zikubwera.
2. Zaka zochuluka kufikira 1996, zozadza ndi kupita patsogolo ndi kuphunzira kwapaokha, kunatsimikizira kuti chiwerengero chachikulu cha anthu mmadera ambiri chikhala chokonzeka kulowa mu Chipembedzo. Komabe, ngakhale chiwerengero chachikulu cha anthu olowa chinali cholimbikitsa chotere, sichinagwirizane ndi ndondomeko ya kukula yopitilira yomwe ikanapezeka mmalo osiyana-siyana. Mbumba inakumana ndi mafunso ozama amene, panthawi imeneyo, panalibe upangiri okwanira kuwayankha molondola. Kuyesetsa komwe cholinga chake chinali kukulitsa kukanapitilira bwanji mbali ndi mbali ndi ndondomeko ya kulimbitsa ndi kukonza zotchinga zapakanthawi ndi zooneka zovuta za kupititsa patsogolo kukula? Kodi anthu, zikhadzikitso ndi mbumba zikanadzutsidwa bwanji zokhala ndi kuthekera kotanthauzira ziphunzitso za Bahá’u’lláh mu ntchito? Ndipo kodi iwo amene anakopeka ndi ziphunzitso akanakhala bwanji otenga mbali mu ntchito yauzimu yadziko lonse?
3. Zinali chonchi kuti, theka la theka ya zaka 100 zapitazo, mbumba ya chi Bahá’í yomwe imatha kuwerengera Manja a Chipembedzo cha Mulungu atatu kutsogolo kwake inayamba ulendo wa Pulani ya Zaka Zinayi, yosiyana ndi mapulani omwe anabwera m’mbuyomo potsindika pa cholinga chimodzi: kupita patsogolo kwakulu pa ndondomeko yolowa mwaunyinji. Cholinga ichi chinafotokozera mndandanda wa Mapulani omwe anatsatira. Mbumba inali itamvetsetsa kale kuti ndondomeko iyi sinali kulowa mu Chipembedzo kwa magulu ocheperapo, kapena kuti iyamba payokha-yokha; zimatanthauza kukulitsa ndi kulimbitsa kwa cholinga, kwadongosolo ndi kofulumira. Ntchito iyi idzafunika kutenga mbali kodziwitsidwa bwino kwa mizimu yaochuluka, ndipo mu 1996, dziko la chiBahá’í lidamemedwa ku ntchito yayikulu yakuphunzitsa. Inayitanidwa kuti ikhadzikitse kulumikizana kwa ma insitichuti osulira anthu olunjika popeza chiwerengero chochuluka cha anthu odzozedwa ndi maluso ofunikira opititsa patsogolo ndondomeko ya kukula.
4. Abwenzi anayiyamba ntchitoyi ndi kuzindikira koti, poyang’anira zipambano zawo zam’mbuyo mu ntchito ya kuphunzitsa, makamaka anayenera kuphunzira za maluso amene amayenera kupeza ndiponso, kwakulu, momwe angawapezere malusowo. Munjira zambiri, mbumba zimatha kuphunzira pochita, ndipo maphunziro omwe imaphunzira, pomwe anasefeka ndi kukonzedwa powagwiritsa ntchito mmalo osiyana-siyana popita nthawi, adzayikidwa mu zipangizo zophunzilira. Panaoneka kuti zochita-chita zina zinali yankho lopezekeratu ku zofunikira zauzimu za unyinji. Masitade seko, makalasi a ana, mapemphero apamodzi, ndipo kenako magulu a achinyamata achisodzera zinaoeneka kufunika kwambiri kumbali iyi, ndipo pomwe zibweretsedwa pamodzi ndi zochitika-chitika zolumikizana, mphamvu zomwe zingatuluke zitha kupereka patani yamphamvu ya moyo wa mbumba. Ndipo pomwe chiwerengero cha anthu otenga mbali chimakula, mbali ina yatsopano inaonjezeredwa ku cholinga chawo chenicheni. Anabwera kudzatumikira ngati zipata zomwe achinyamata, akulu ndi maanja onse kuchokera ku mbumba yayikulu adzabwera ndi kukumana ndi Chibvumbulutso cha Bahá’u’lláh. Zinayamba kuonekanso momwe kunalili kotheka kuganizira njira zomwe ntchito yomanga mbumba mu kalasita: kadera kakakulupo kokhala ndi chikhalidwe ndi machitidwe a ntchito zachitukuko ndi chuma zofanana, kunalili kotheka. Kuthekera kokonzekera mapulani apafupi pa kalasita kunayamba kupezeka, ndipo kuchokera mu mapulani otere, maplogalamu a kukula kwa Chipembedzo anadzuka, olongosoledwa kukhala zomwe zinatchulidwa pambuyo pake mapulani a zochitika-chitika za miyezi itatu. Mbali imodzi yofunikira kutambasula inaoneka poyambilira pomwe: kuyenda kwa anthu mu mndandanda wa maphunziro a insitichuti kumapereka mangolomera ku, ndipo kumapitilizidwa ndi, kusuntha kwa makalasita pa mndandanda wa chitukuko. Ubwenzi uwu olumikizana unathandiza abwenzi ponse-ponse kuona momwe mbali za kukula mmalo owazungulira ndi kukonza njira ya mphamvu zopitilira. Pomwe nthawi imapita, panaoneka phindi kuona zomwe zimachitika mu kalasita kuchokera ku mbali zonse ziwiri za malamulo atatu a kuphunzira—kutumikira ana, achinyamata achisodzera, achinyamata ndi akulu—komanso kumbali ya masayiko a zochitika-chitika zofunikira ku mlingo wa kukula. Kulowa pang’ono mu ntchito za gawo la zaka makumi awiri ndi zisanu, zambiri mwa zinthu zomwe zinaoneka pa ndondomeko ya kukula komwe tikuona lero kunayamba kukhadzikika bwino.
5. Pomwe ntchito za abwenzi zimakula, mfundo zosiyana-siyana, njira ndi kachitidwe kofunikira ku ndondomeko ya kukula kunayamba kuwumbika mu dongosolo la ntchito lomwe lidzasintha ndikulora mbali zina zatsopano kukonzedwa. Dongosolo ili linaoneka kuti ndi lofunika pofuna kutulutsa mphamvu zamtundu wina. Zinathandiza abwenzi kulunjikitsa mphamvu zawo munjira zimene, upangiri unaonetsa kuti, zinali zofunikira ku kukula kwa mbumba za nthanzi.
Koma dongosolo si njira. Poyang’anira mbali zosiyana-siyana za dongosolo powunikira uweniweni wa kalasita, dera, kapena, dera lowandikana, patani ya chochitika itha kupangidwa yomwe ingalunjike pa zimene dziko lonse lachiBaha’i limaphunzira pomwe likukhalanso yankho ku zofunikira za dera limenelo. Kutsutsana pakati pa zofunikira zokakamira ndi kupanda malire pa zomwe munthu akudzikonda kunapereka njira yomvetsetsa yabwino ya kachitidwe kosiyanasiyana komwe anthu atha kuthandizira ndondomeko imene, pamtima pake, inali yololera mbali zonse ndi imene ikupitilirabe kuyikonza pomwe upangiri ukuchuluka. Pasakhale kukayika kulikonse pa kupita patsogolo komwe kunaperekedwa pachiyambi cha dongosolo ili: zotsatira zoluzanitsa ndi kuyanjanitsa ntchito za dziko lonse la chiBahá’í ndi kusonkhedzera kupita patsogolo kwake kunali zotsatira zazikulu.
6. Pomwe Pulani ina imayamba pambuyo pokutha kwa ina ndipo kulumikizana ndi ntchito yomanga mbumba imaonekeratu yokhazikika, zofunikira pa mlingo wa chikhalidwe unayamba kuoneka. Mwachitsano, kufunikira kophunzitsa mibadwo yachichepere kunayamikiridwa kwambiri, monga momwe kunaonekeranso kuthekera kwa achinyamata achisodzera makamaka. Mizimu yothandizana ndi kuyendera pamodzi panjira yogawana, kukulitsa sayiko ya kuthandizana, inakhala patani yomwe kuyesetsa kolunjika pa kutulutsa maluso otumikira kunapezedwa. Ngakhale kuchezerana kwa abwenzi akati pawo ndi iwo amene anawazungulira zinasintha, pomwe kuzindikira kunakwezedwa kwa mphamvu ya kukambirana kwa tanthauzo kuyatsa ndikuthandizira zofooka zauzimu. Ndipo chapamwamba kwambiri, mbumba za chiBahá’í zinatenga njira yapamtunda yolumikizanirana. Mzimu ulionse ovomera masomphenya a Chipembedzo umatha kukhala wotenga mbali wamphamvu—ngakhale wopititsa patsogolo kapena woyendetsa—wa zochitika-chitika za maphunziro, mikumano yopembedzera ndi mbali zina za ntchito yomanga mbumba; kuchokera mu mizimu imeneyi, ambiri amavomera chikhulupliro chawo mwa Bahá’u’lláh. Ndiko kuti, ganizo la ndondomeko ya kulowa mwaunyinji inayamba yomwe inadalira pang’ono pa zolankhula ndi zoganizira ndi kwambiri pa upangiri wopezeka wa momwe chiwerengero chachikulu cha anthu chingapezere Chipembedzo, kuchidziwa, kudzifanizira okha ndi zolinga zake, kuchita nawo zochita-chita zake ndi zokambirana, ndipo nthawi zambiri kuchilandira icho. Indetu, pomwe ndondomeko ya institichuti imalimbitsidwa mu chigawo ndi chigawo, chiwerengero cha anthu omwe amatenga nawo gawo mu ntchito ya Pulani, kufalikira ngakhale kwa iwo omwe anangodziwa kumene za Chipembedzo, chinakula kwambiri. Koma izi sizinachitike pongofuna kuchulukitsa chiwerengero. Masomphenya a munthu payekha ndi kusinthika kwa anthu onse kooneka nthawi imodzi, kopezeka pa kuwerenga Liu la Mulungu ndi kuyamikira kwa kuthekera kwa munthu wina kukhala wotenga mbali atatu mu sewero lozama zauzimu, kunapereka kuzindikira kwa ntchito ya cholinga chimodzi.
7. Chimodzi mwa zinthu zopatsa chidwi ndi zolimbikitsa mu nyengo ya zaka makumi awiri ndi zisanu izi ndi kutumikira komwe achinyamata a chiBaha’i anapereka, omwe ndi chikhulupiliro ndi kulimba mtima kwakulu pakati pa zolepheretsa zambiri apeza malo awo oyenelera patsogolo pa kuyesetsa kwa mbumba. Monga aphunzitsi a Chipembedzo ndi asuli a achichepere, ngati aphunzitsi oyenda-yenda ndi mapayoniya akudera lowandikana nalo, ngati makodineta a kalasita ndi mamembala a nthambi za chiBaha’i, achinyamata amakontineti asanu adzuka ndi kutumikira madera awo ndi kudzipereka ndi kudzikhuthura. Kukhwima mu nzeru komwe awonetsa, pogwira ntchito yomwe kupita patsogolo kwa Pulani Yoyera kukudalira, ndi chiwonetsero cha mphamvu zauzimu zawo ndi kudzipereka kwawo poyang’anira bwino tsogolo la mtundu wa anthu. Pozindikira kukhwima mu nzeru kopitilira uku, taganiza kuti, nyengo yotsatira Rizwani iyi, pomwe zaka zimene wokhulupilira atha kuloledwa kutumikira pa zikhadzikitso zikhalabe 21, zaka zimene wokhulupilira angathe kuvota m’masankho a chiBaha’i zatsitsidwa kufika pa 18. Tilibe kukayika kulikonse kuti achinyamata achiBahá’í kulikonseko omwe ali pa msinkhu umenewu atitetezera pa chikhulupiliro chathu mu kuthekera kwawo kukwaniritsa “mosamala ndi mosaopa”
“udindo wopatulika” omwe m’Bahai ovota aliyense wayitanidwa.
*
8. Tikuzindikira kuti, mwachilengedwe, mauweni-weni a madera amasiyana kwambiri. Mbumba zamdziko zosiyana-siyana, ndi malo osiyana-siyana mu mbumba zimenezo, anayamba mndandanda uwu wa Mapulani panthawi zosiyana-siyana za chitukuko; kuyambira pamenepo, apitanso patsogolo pa mlingo wosiyana-siyana ndipo akwaniritsa milingo yosiyana-siyana ya kupita patsogolo. Ichi, mwa icho chokha, sichachilendo. Zakhala chomwechi kuti zochitika mmalo zimasiyana, monga momwe mlingo wa malandilidwe umapezekera kumeneko. Koma tikuonanso, funde lalikulu, pomwe kuthekera, kudzikhulupilira ndi upangiri wochuluka wa mbumba zambiri ukupitira patsogolo, mokwezedwa ndi chipambano cha mbumba zoyandikana nazo ndi zapatali. Monga mwachitsanzo, pomwe mizimu yomwe inadzuka ndi kutsegula dera latsopnao mu chaka cha 1996 sanasowe chilichonse pa kulimba mtima, chikhulupiliro ndi kudzipereka, lero amnzawo kulikonse akuphatikiza makhalidwe omwewa ndi kuzindikira, kuphunzira ndi maluso omwe akhala akusonkhanitsidwa mu zaka makumi awiri ndi zisanu za kuyesetsa kwa dziko lonse la chiBahá’í world kulongosola ndi kukonza ntchito ya kukulitsa ndi kulimbitsa.
9. Posayang’anira kuti dera layambira pati, Lapititsa patsogolo ndondomeko ya kukula pomwe yaphatikiza makhalidwe a chikhulupiliro, kupilira ndi kudzipereka ndi kukonzekera kuphunzira. Motsindika, nkhani yonyaditsa mu mndandanda uwu wa Mapulani ndi kuzindikira kofalikira kuti kuyesetsa kopita patsogolo kumayamba ndi khalidwe la kuphunzira. Kuphweka kwa mfundo iyi kukutsutsa kufunika kwa zotsatira zomwe zimachokera mu ichi. Sitikukayika kuti mu kalasita iliyonse, itapatsidwa nthawi, idzapita patsogolo pa mndandanda wa chitukuko; mbumba zomwe zapita patsogolo mofulumira, mogwirizana ndi izo zomwe uweni-weni ndi kuthekera kwake kunali kofanana, zaonetsa kuthekera kobweretsa umodzi wa kaganizidwe ndi kuphunzira kufunika kw ntchito yadongosolo. Ndipo anapanga choncho popanda kukayika kuchitapo kanthu.
10. Kudzipereka ku kuphunzira kumatanthauzanso kukhala okonzeka kulakwitsa-ndipo nthawi zina, inde, kulakwitsa kumabweretsa madandaulo. Mosadabwitsa, njira zatsopano ndi machitidwe a zinthu sizinakonzedwe bwino koyambirira Kamba kosowa upangiri; pa nthawi ina; kuthekera kwatsopano kumatayika pomwe dera linali lotangwanika ndi kutumikira lina. Kukhala ndi malingaliro abwino si chitsimikizo kuti kulakwitsa sikungachitike, ndipo kuphunzira pa kudutsa apo kumafunika kudzichepetsa ndi kudzipatula. Pomwe dera lakhala lochilimika kuonetsa kupilira ndi kuphunzira mu kulakwitsa kwake komwe sikulephera, kupita patsogolo sikunalepherekepo.
11. Pakati-kati mu mndandanda wa Mapulani, kukhudzika kwa mbumba mu moyo wa dera kunayamba kukhala mbali yoonetserapo chidwi chachikulu. Okhulupilira analimbikitsidwa kuganizira izi kumbali ziwiri za ntchito zolumikizana—ntchito ya chitukuko ndi kutenga gawo mu zochitika-chitika za dera zofalikira. Izi, indetu, zinali mbali zina za ntchito ya kukulitsa ndi kulimbitsa, osati zosokoneza: zinali mbali imodzi yochokera mu ntchito imodzi. Kuchuluka kwa chiwerengero cha otumikira komwe dera limadalirapo, kudabweretsa kukula kwa kuthekera kwake kubweretsa nzeru zopezeka mu Chibvumbulutso cha Bahá’u’lláh polimbana ndi mavuto a tsiku lalero. Ndipo mavuto a mtundu wa anthu mu nyengo imeneyi kunaonetsa kufunikira kwa mankhwala ake ochiza operekedwa ndi Mchiritsi Woyera. Zomwe zimatanthauza mu zonsezi chinali chiyambi cha chipembedzo chosiyana ndizomwe ndi zodziwika padziko lonse lapansi: chiyambi chomwe chinazindikira chipembedzo ngati mphamvu yothamangitsa chitukuko chopitilira. Zinali zodziwika kuti kusinthika kotere sichionekera mwadzidzi, mwa kufuna kwake— inali ntchito ya otsatira Bahá’u’lláh kugwira ntchito kuti kusinthikaku kuonekere. Ntchito yotere inafunika kugwiritsa ntchito ndondomeko yomweyo ya kuphunzira kwa dongosolo ku ntchito ya chitukuko ndi kutenga mbali mu ntchito zokhudza onse.
12. Poyang’anira zamu zaka makumi awiri ndi zisanu, kuthekera kogwira ntchito zachitukuko kwakwera kwambiri, kupangitsa kufalikira kofulumira kwa ntchito. Poyerekeza ndi 1996, pomwe ntchito za chitukuko zokwana 250 zinapitilira chaka ndi chaka, tsopano alipo 1,500, ndipo chiwerengero cha zikhadzikitso zoyambitsidwa ndi aBaha’i chakula kudutsa 160. Ntchito zachitukuko za m’madera zoposa 70,000 za kanthawi kochepa zikuchitika chaka chilichonse, kukwera ndi makumi asanu. Tikuyembekezera kukwera kwa chiwerengero cha ntchito zimenezi kuchokera ku mathandizo odzipereka ndi mangolomera omwe tsopano akuperekedwa ndi
Chikhadzikitso Chachikulu chachiBaha’i pa Chitukuko (Bahá’í International Development Organization). Pakali pano, kutenga mbali kwa aBahá’í mu ntchito za chitukuko zomwe panopa zafalikira ponse ponse kwapita patsogolo. Pambali pa miyayi yochuluka pomwe abwenzi akumapereka mbali ya chiBaha’i mu zokambirana zomwe zimachitika malo a ntchito kapena pochezerana, kutenga nawo mbali kwa dongosolo mu zokambiranazi kwapitanso patsogolo kwambiri. Tikuganizira ntchito zofalikira osati za Mbumba YachiBaha’i Yakunja yokha—imene munyengo imeneyi yawonjezera maofesi ku Afirika, Asia ndi Europe—komanso ntchito yogwiridwa bwino ndi chilumikizo chachikulu chama ofesi a zochitika kunja kwadziko la chiBaha’i (External Affairs), omwe gawo ili la ntchito linakhala lofunikira; kuonjezera, panali maphunziro ndi zosonkhera zooneka zoperekedwa ndi okhulupilira paokha-paokha ku mbali zina zapadera zonsezi zikupita ku chifotokozo chachikulu, kuthokoza ndi kuyamikira komwe atsogoleri oganiza ndi ena odziwika pamilingo yonse ya dera awonetsa mobwereza-bwereza kwa Chipembezo, otsatira ake ndi ntchito zawo.
13. Powunika zaka 25 zonse, tili ozizwa ndi kupita patsogolo kosiyana-siyana komwe dziko lachiBaha’i lakwaniritsa pakamodzi. Moyo wake wa maphunziro wapiti patsogolo, osati pongotengera ntchito zake zomwe zakambidwa kale, komanso kuchuluka kwa zolemba-lemba zosindikizidwa ndi olemba za chiBaha’i, kupita patsogolo kwa mipata yofufuza mbali zina zokhudzana ndi chiphunzitso, ndinso kutukuka kwa seminale za maphunziro a chitukuko operekedwa ndi Insitichuti ya Maphunziro a Chitukuko cha Dziko lonse kwa achinyamata a msukulu zaukachenjede omwe anamaliza ndinso omwe akuphunzirabe , omwe, mogwirizana ndi zikhadzikitso za Chipembedzo, tsopano akutumikira achinyamata ochokera mmaiko osachepera 100. Kuyesetsa kamanga Nyumba Zopembedzeramo kwapitanso patsogolo kwambiri. Nyumba yomaliza Yopembedzeramo inamangidwa ku Santiago, Chile, ndi pulani yofuna kumanga nyumba ziwiri za m’dziko zotumikiramo ndi zina zisanu m’madera inayambika; Nyumba Yopembedzeramo ku Battambang, Cambodia, ndi Norte del Cauca, Colombia, zatsegulidwa kale. Nyumba Zopembedzeramo, kaya zatsopano kapena zakale, zikupitilira kutenga mtima wa moyo wa mbumba. Thandizo la katundu operekedwa ndi okhulupilira ku ntchito zochuluka zomwe abwenzi a Mulungu akugwira lakhala lochuluka. Ngati ntchito yapafupi yapamodzi ya kutukuka kwa uzimu. Kudzipereka ndi kudzikhuthura komwe, panthawi ya msautso wa zachuma, kusonkhera kuthumba kwakhala kopitilira –indedi, kolimbitsidwa- mosaneneka. Mu khalidwe la kayendetsedwe ka chiBaha’i, kuthekera kwa Mabungwe Auzimu Aakulu kukwaniritsa zofuna za mbumba zawo ku mbali zonse kwapititsidwa patsogolo. Apindula mwapadera kumbali ziwiri zapamwamba za kugwilira ntchito limodzi ndi maKhansala, ameme akhalanso zida zodalilika mobweretsa dongosolo la kutolera zophunziridwa kuchokera ku madera padziko lonse ndi kuonetsetsa kuti zikugawidwa ponse ponse. Iyinso inali nyengo momwe Makhonsolo a Mzigawo anatuluka kukhala zikhadzikitso zodziyimira pazokha za Chipembedzo, ndipo zikupezeka mzigawo zokwana 230 tsopano, makhonsolo ndi ma insitichuti ophunzitsa omwe akuyang’anira zaonetsa zokha kuti ndi zofunikira popititsa patsogolo ndondomeko ya kukula. Pofuna kutambasulira mtsogolo ntchito za Wamkulu Woyang’anira Ḥuqúqu’lláh, Dzanja la Chipembedzo cha Mulungu ‘Alí-Muḥammad Varqá, Bodi yayikulu ya Woyang’anira Ḥuqúqu’lláh inakhadzikitsidwa mu chaka cha 2005; lero ikulumikizitsa kuyesetsa kwa woyang’anira a mzigawo zosachepera 33 ama Bodi a mmaiko ndinso mzigawo padziko lonse, omwe mmalo mwake akutsogolera ntchito ya Woyimira opitilira 1,000. Zitukuko zomwe zinachitika ku Malo Oyera mu nyengo imeneyi ndi zambiri: tinachitira umboni kumalizitsa kwa masitepe (Terraces) a Malo Owusirako a Báb ndi nyumba ziwiri ndi kuyambika kamanga Nyumba Yowusiramo ya
‘Abdu’lBahá, osayiwala ntchito zina zolimbitsa ndi kuteteza Malo Oyera a Chipembedzo. Malo Owusira a Bahá’u’lláh Báb anazindikiridwa ngati amodzi mwa malo ozizwitsa (World Heritage) padziko lonse, malo a mtengo wapatali ku mtundu wa anthu. Anthu amathamangira ku malo opatulikawa mu unyinji wawo, kufika pafupi-fupi theka la miliyoni zaka zina, ndi Sentala ya Dziko lonse imalandira alendo mazana pakamodzi, nthawi zina kudutsa 5,000 m’chaka chimodzi, kuphatikizapo alendo achiBahá’í; ndife wokondwa pa chiwerengero chochuluka monga momwenso tilili okondwa ndi ndi mitundu ya anthu osiyana-siyana ndi maiko omwe amayimira pakati pa iwo amene amabwera ku ulendo woyera (pilgrimage). Kumasulira, kusindikiza ndi kutumiza mbali zonse kwa Malembo Woyera kwapitanso patsogolo, pamodzi ndi kupititsa patsogolo kwa Nkhokwe ya Malembo a chiBaha’i (Bahá’í Reference Library), imodzi mwa nkhokwe zapa intaneti zolumikizana ndi Bahai.org, yomwe mwa iyo yokha tsopano ikupezeka mu ziyankhulo zokwana khumi. Mitundu ya maofesi yosiyana-siyana ndi nthambi zina zakhadzikitsidwa, ku Malo Oyera ndinso madera ena, zothandizira ndondomeko ya kuphunzira komwe kukutambasuka mbali zosiyana-siyana za ntchito mdziko lonse la chiBaha’i. zonsezi, abale andi alongo athu mu chikhulupiliro, ndipang’ono chabe mwa nkhani zomwe tingakambeko za zomwe kudzipereka kwanu kwa Iye Amene anali Wolakwiridwa wa Dziko Lapansi anabweretsa.
Titha kungobwerezako mawu oswetsa mtima omwe ananenapo Abdu’l-Baha pamene, atakhudzika kwakukulu analira mokweza: “O Bahá’u’lláh! Mwachitanji?”
*
14. Pamwamba pa kota ya zaka zana limodzi, tsopano tionetsetse pa Pulani ya Zaka Zisanu yomwe yangothayi, Pulani yosafanirizika ndi ina iliyonse munjira zosiyana-siyana. Mu Pulani iyi tidamema aBaha’i a dziko lapansi kuti atute zonse zomwe adaphunzira mu zaka makumi awiri zapita ndi kuzigwiritsa ntchito mokwanira. Ndife okondwa kuti ziyembekezo kumbali iyi zinadutsa mlingo wokwaniritsidwa, komabe pomwe mwachidziwikire tikuyembekeza zinthu zazikulu kuchokera kwa Otsatira a Wokongola Wodalitsikayo, maonekedwe a zomwe zinakwaniritsidwa kudzera mu kugwira ntchito modzikhuthura kunali kotenga mtima. Inali Tsonga la chimake cha chikwanilitso cha zaka 25.
15. Pulani inali yapadera ndi chikumbukiro cha zikondwelero zoyera ziwiri, chilichonse mwa izi chinabweretsa moto wapadera ku mbumba padziko lonse. Gulu la wokhulupirika linaonetsa, pa mlingo omwe sunaonekenso ndi mosavuta, kuthekera kokhudza anthu a mbali zonse polemekeza moyo wa m’Bvumbulutsi wa Mulungu. Chinali chizindikiro cha chinthu chinachake chachikulu: kuthekera kobweretsa pamodzi kutuluka kwa mphamvu zauzimu pa kupita patsogolo pa Chipembedzo. Kulandiridwa kwake kunali kopambana mwakuti mmadera ambiri Chipembedzo chinadziwika pamlingo wadziko. Mmalo ena momwe sizinayembekezeke, kapena kusang’anirapo, kulandira kwa anthu kwa Chipembedzo kunali koonekeratu. Mazana ndi mazana ndi mazana a anthu anatengedwa ndi kukumana kwa mzimu wa pemphero omwe lero ndi chizindikiro cha mbumba zachiBaha’i kulikonse. Masomphenya a chomwe chimapangidwa kutheka posangalalira Tsiku Loyera la chiBaha’i anakulitsidwa kwambiri.
16. Chipambano cha Pulani, mu nambala zomveka bwino, chinadutsa mofulumira awo onse a Mapulani a kumbuyo chiyambireni 1996. Pomwe Pulani iyi imayamba, panali kuthekera kopanga zochitika-chitika zopitilira 100,000 panthawi, kuthekera komwe kunali chipatso cha zaka 20 za ntchito yapamodzi. Tsopano zochitika-chitika zoposa 300,000 zikuchitika. Kutenga mbali mu zochitika-chitika zimenezi kwadutsa pa mamiliyoni awiri, kukwera patatu. Pali zikhadzikitso za insitichuti mmako ndi mzigawo zokwana 329 zomwe zikugwira ntchito, ndipo kuthekera kwawo kukuonekera mu umboni wakuti tsopano anthu okwana mazana 750 akwaniritsa kumalizitsa buku limodzi pa mndandanda wa mabuku a insitichuti; onse pamodzi, chiwerengero cha makozi omwe amalizidwa ndi anthu tsopano chili mamiliyoni awiri kukwera pafupi-fupi ndi theka ndi kota mu zaka zisanu.
17. Kukula kwa kutsindika komwe mapologalamu a kukula a kathithi akuchitidwira kukufotokoza nkhani yosangalatsa paokha. Mu zaka zisanu izi, tidapempha kuti kukula kwa kathithi kufalikire mu makalasita okwana 5,000 omwe kudayamba kale. Chitsogozo ichi chidakhala mangolomera ogwira ntchito modzipereka padziko lonse. Zotsatira zake, chiwerengero cha makalasita omwe ali ndi pologalamu ya kukula mwakathithi chidawonjezereka kwakulu tsopano chili pafup-fupi 4,000. Zovuta zomwe zinapezeka potsegula midzi ndi madera owandikana atsopano ku Chipembedzo mkatikati mwa chipwilikiti cha matenda padziko lonse, kapena kukulitsa zochitika-chitika zomwe zinali zosakhazikika pomwe mliri umayambika, zinalepheretsa kuti chiwerengero chachikulu chikwaniritsidwe mu chaka chomaliza cha Pulani. Komabe, pali zambiri zoti zikambidwe kuposa izi. Poyambilira pa Pulani, tidafotokoza chiyembekezo kuti chiwerengero cha makalasita komwe abwenzi anadutsa mtunda wachitatu (IPG) pa mndandanda wa kukula, ngati chotsatira chophunzira momwe angalandilire chiwerengero chochuluka mu zochitika-chitika zawo, chidzakula ndi mazana owonjezera. Chiwerengero chimenechi nthawi imeneyo chinali pa 200, m’maiko pafupi-fupi. Zaka zisanu zadutsapo, chiwerengero ichi Chakwera kufika pa 1,000 m’maiko pafupi-fupi 100—kota ya mapologalamu onse a kukula mwakathithi m’dziko lonse, chikwaniritso chomwe chadutsa chiyembekezo chathu. Koma ngakahle chiwerengero ichi sichikuwulura utali omwe mbumba zafikirapo. Pali makalasita oposa
30 komwe chiwerengero cha zochitika-chitika zomwe zikupita patsogolo zikudutsa 1000; m’malo, chiwerengero chonse chikukwana mazana-mazana, kuphatikiza kutenga mbali kwa anthu opitilira 20,000 mu kalasita. Chiwerengero chokwera cha Mabungwe Auzimu Aang’ono tsopano akuona kutambasuka kwa mapologalam a maphunziro omwe akutumikira kwa ana onse ndi achinyamata achisodzera; izinso zayamba kuoneka m’madera ena a mmizinda. Kukumana ndi Chibvumbulutso cha Bahá’u’lláh, kwapangitsa, pa zitsanzo zooneka, kukweza anthu, maanja ndi abale ena— zomwe zikuoneka mu kuyenda kwa unyinji kulunjika ku cholinga chapamodzi. Nthawi zina, kusamvana kwakale-kale pakati pa magulu awiri otsutsana kukusiyidwa pambuyo, ndipo ntchito zina za dera ndi mphamvu zina zikusinthika potsatira kuwala kwa ziphunzitso zoyera.
18. Sitingakhale osakondwa pa zinthu zonyaditsazi. Mphamvu zomanga dera za Chipembedzo cha Bahá’u’lláh zikutulutsidwa ndi kutambasuka kwakukulu, ndipo awa ndi maziko olimba pomwe Pulani ya Zaka Zisanu ndi Zinayi ikubwerayi idzamangidwapo. Makalasita a mphamvu zodziwika, monga momwe kunayembekezeredwa, akhala nkhokwe za kuphunzira ndi mathandizo kwa owandikana nawo. Ndipo zigawo komwe makalasita oterewa adutsa imodzi apititsa patsogolo mosavuta njira zothamangitsira kukula mu kalasita ndi kalasita. Tili okakamizidwa kutsindika kawiri, komabe, kuti kupita chitsogolo kwafalikira, kusiyana pa kupita patsogolo pakati pa malo amodzi ndi ena ndikwa muyeso. Kumvetsetsa kwapamodzi kwa mbumba pa ndondomeko ya kulowa mwaunyinji ndi kudzikhulupilira kwake pokwaniritsa kulimbikitsa ndondomeko imeneyi mu nyengo zina zilizonse kwakwera kufika pa mlingo omwe sunaganiziridwe ndikale lonse. Mafunso ozama omwe anakhala akutuluka kwa nthawi yayitali, ndi omwe anayikidwa mu chindunji mu chaka cha 1996, akhala akuyankhidwa mokhutira bwino ndi dziko la chiBaha’i. pali m’badwo wa okhulupilira omwe miyoyo yawo yonse akhala akuchitira umboni kupita patsogolo kwa mbumba. Koma mlingo waukulu wa zimene zachitika mmakalasita ochulukawa komwe danga la kuphunzira lakhadzikitsidwa lakulitsa kwambiri ndondomeko ya kulowa mwaunyinji kukhala yofunikira ya magawo a mbiri.
19. Ambiri akukumbukira momwe Mtchinjilizi anagawira Ndime za Chipembedzo mu magawo otsatana; gawo loyamba ya Ndime Yomanga linayamba chaka cha 2001. Zomwe zikudziwika pang’ono ndi zoti Mtchinjilizi anapereka umboni kuti kuli magawo a Pulani Yoyera, ndi ndime mkati mwa magawo amenewo. Zinayimitsa kwa zaka makumi aiwiri pomwe zikhadzikitso za mmadera ndi mmaiko za Ndondomeko ya Kayendetsedwe zimakhadzikitsidwa ndi kulimbitsidwa, Pulani Yoyera yokonzedwa ndi ‘Abdu’l-Bahá inakhadzikitsidwa mu chaka cha 1937 ndi kuyambika kwa ndime yoyamba ya gawo loyamba: Pulani ya Zaka Zisanu ndi Ziwiri (7) yokhadzikitsidwa ndi Mtchinhilizi ku mbumba ya chiBaha’i yakumpoto kwa Amerika. Gawo loyamba linatsekedwa kumapeto a Zaka Khumi za Kampeni muchaka cha 1963, yomwe zotsatira zake zinali kudzalidwa kwa mbendera ya Chipembedzo padziko lonse. Ndime yotsegulira ya gawo lachiwiri ina Zaka Zisanu ndi Zinayi (9) zoyambilira, ndipo ma Pulani osachepera khumi anatsatira, Mapulani omwe anali a zaka zapakati pa chimodzi ndi zisanu ndi ziwiri (7). Poyambilira pa gawo ili lachiwiri, dziko la chiBaha’i linali litaona kale chiyambi cha kulowa mu Chipembedzo mwaunyinji komwe Mlembi wa Pulani Yoyera analosera kale; mu zaka zotsatira, mibadwo ya okhulupilira odzipereka mu mbumba ya Dzina Lalikulu Koposa agwira ntchito mu Munda Woyera kubzala zoyenelera kubweretsa kukula kwakukulu kopitilira. Ndipo pa nyengo ino yaulemelero ya Rizwani, zipatso zimenezi ndi zochuluka bwanji! Kuonekera kwa chiwerengero chabwino chomwe chikutenga mbali mu zochita-chita za mbumba, kugwira kuwala kwa chikhulupiliro ndi kudzuka ndi kutumikira mofulumira kumayambiliro a Pulani yachoka pa chidwi chobwera ndi chikhulupiliro ndipo tsopano ndi choonadi chobwerezabwereza. Kupita patsogolo koonekeratu ndi kolozeka uku kukufuna kuzindikiridwe mu mabuku a Chipembedzo. Ndi mitima yosangalala, tikulengeza kuti gawo lachitatu la Pulani Yoyera ya Mtchinjilizi yayamba. Ndime ndi ndime, gawo ndi gawo Pulani yake imasulidwa, mpaka kuwala kwa Ufumu kuwalitse mtima ulionse.
20. Abwenzi okondedwa, kuunikira kwa ntchito ya zaka zisanu yomwe yamalizitsa ndime yachiwiri ya Pulani Yoyera kukhala kosakwanira popanda kutchulapo zovuta zomwe zinaperekeza mu chaka chomaliza zomwe zikupitilira mpaka pano. Kuletsa kuchitira zinthu pamodzi kwa anthu komwe kunakula ndi kuchepa mmaiko ambiri mu nyengo imeneyi kukanatha kugwetsa kuyesetsa kwa pamodzi kwa mbumba, komwe kuchira kwake kukadatenga zaka, koma pali zifukwa ziwiri zomwe izi sizidakhalire chomwecho. Choyamba kunali kukhudzika kofalikira kwa udindo wa aBaha’i kutumikira mtundu wa anthu, mochuluka kuposa mu nthawi ya masautso ndi mavuto. Chawiri chinali kudzuka kodabwitsa mu kuthekera kwa dziko la chiBahá’í poyankhapo pa kukhudzika kumeneku. Chizolowezi cha zaka zambiri chophunzira patani ya kugwira ntchito mwa ndondomeko, abwenzi anabweretsa maluso awo ndi ganizo la cholinga kukwaniritsa kunyamula chionongeko chosakonzekereka, kwinaku akuonetsetsa kuti njira zatsopnao zomwe akugwiritsa ntchito zinali zogwirizana ndi ndondomeko zomwe anayesetsa mu ma Pulani akumbuyo kudzisula kuti zikhale zangwiro. Ichi sikufuna kupepusa zovuta zazikulu zomwe aBaha’i akukumana nazo, monga akuchitira amnzawo padziko lonse; komabe mu nyengo ya zovuta zawo yonse, okhulupilira akhala oima njii. Mathandizo aperekedwa ku mbumba zomwe zimafuna thandizo, masankho anachitika komwe kunali kuthekera, ndipo mu nyengo zonse zikhadzikitso za Chipembedzo zapitilira kugwira ntchito zawo. Pakali pena kutenga ndime zikulu-kulu popita chitsogolo. Bungwe Lauzimu Lalikulu la São Tomé ndi Príncipe likhadzikitsidwanso mu nyengo iyi ya Rizwani, ndipo nsanamira zina ziwiri ya Nyumba ya Chilungamo ya Amitundu zidzutsidwa: Bungwe Lauzimu Lalikulu la Croatia, ndi likulu la ku Zagreb, ndi Bungwe Lauzimu Lalikulu la Timor-Leste, ndi likulu lake ku Dili.
21. Tsopano Pulani ya Chaka Chimodzi yayamba. Cholinga ndi zofunikira zake zinafotokozedwa kale mu uthenga wathu womwe unatumizidwa pa Tsiku la Pangano; Pulani iyi, ngakhale yayifupi, ikwaniritsa kukonzekeretsa dziko la chiBahá’í ku Pulani ya Zaka 9 yomwe itsatire. Nyengo ya mphamvu zapadera, yomwe inatsegula zaka 100 pomwe ma Tabuleti a Pulani Yoyera anavumbulutsidwa, itsekedwa posachedwa ndi zaka 100 zakukwera kumwamba kwa ‘Abdu’l-Bahá, kukwaniritsa mathero a zana loyamba la Nyengo Yomanga (Formative Age) ndi kuyambika kwa yachiwiri. Gulu la wokhulupirika likulowa Pulani iyi yatsopano panthawi yomwe mtundu wa anthu, modzichepetsa ndi kufooka kwake ukuoneka kuti ukuzindikira kufunika kogwirana manja pothana ndi mavuto a dziko lonse. Komabe, zizolowezi zopikisana, kudzikonda, tsankho ndi kusamasukirana zikupitilira kusokoneza ulendo wa umodzi, ngakhale chiwerengero chachikulu cha anthu omwe akuonetsa mu mau komanso ntchito momwe iwonso, akufunitsitsa kuvomereza kwakulu kwa umodzi wa anthu wamkati. Tipemphera kuti maanja a dziko lapansi akwaniritse kuyika pambali kusiyana kwawo pofuna kupititsa patsogolo zabwino. Posayang’anira zotchinga zomwe zakutira miyezi ikubwerayi, tikupempha Bahá’u’lláh kulimbitsa chikhulupiliro chomwe chalimbikitsa omtsatira Ake kwa nthawi yayitali kuti chichuluke kuti, mupite patsogolo mu ntchito yanu, kuchilimika kwanu kusasokonezedwe ndi mafunde a dziko amene kufunitsitsa kwakukulu kwa uthenga wochiritsa kuli koonekeratu.
Pulani Yoyera ikulowa nyengo yatsopano ndi ndime yatsopano. Tsamba latsekulidwa.
Tili ndi chimwemwe chachikulu poyankhula ku mbumba yomwe malingaliro ake apamwamba akugwirizana ndi kuyitanidwa kwake kwakukulu. Ndichikondi chachikulu bwanji, inde chachikulu zedi chikondi chathu pa inu, momwe mizimu yathu inthunthumira ndi m’mene tikuona kuyesetsa kwanu kodzipereka ndi kowona mtima, kukhala miyoyo youmbidwa ndi Ziphunzitso za Bahá’u’lláh ndi kupereka madzi opatsa moyo a Chibvumbulutso Chake kudziko la ludzu. Nzeru ya cholinga chanu chachikulu ndiyowonekeratu. Kuphunzitsa ndi kuzamitsa, ntchito za chitukuko, ndikutenga nawo mbali muzokambirana zam’madera zikupita chitsogolo, ndipo limodzi zinthu izi zikuwonekeratu munkwamba. Nkutinso kwina izi zikuwonekera kupambana komwe chiwerengero chachikulu chikuchita ntchito zosiyana-siyana, iri yonse mwa iyo ndi chida chotsanulira mphamvu za Chipembedzo zomanga dera.
Miyezi khumi ndi iwiri yadutsapo chiyambireni Pulani iyi ya zaka Zisanu ndi zinayi, tiri okondwa kuona momwe ntchito yauzimu ya dziko lonse yasunthira ndi kupereka mangolomera kwa abwenzi ndikupereka mphamvu ku mbali zina za ntchito. Mosazengereza, chidwi chinalunjikitsidwa kuika mapulani amene awonetsetse kuti m’dziko ndi m’chigawo chilichonse mutuluke mkwamba umodzi umene wadutsa mtunda wachitatu: malo amene chiwerengero chachikulu cha anthu akugwira ntchito limodzi ndi kusonkhera ku umoyo wa mbumba wotaka-taka. Pozindikira, komabe, kuti golo la zaka makumi awiri ndi zisanuzi ndikukhadzikitsa ndondomeko yakathithi yakukula mu mkwamba uli onse padziko lapansi, okhulupilira ndi okonzekanso kutsegula mikwamba yatsopano ku Chipembedzo komanso kuwonjezera kuyesetsa kwawo m’malo momwe muli kale ndondomeko ya kukula mwa kathithi. Pali kuzindikira kwakukulu zamwayi wakuti akashole (mapayoniya) adzuke mbali zonse za dziko lapansi—khwimbi lamizimu yodzipereka ikulingalira momwe ingadzukire kuchitapo kanthu pa mwayi umenewu, ndipo mizimu ina yambiri yapita kale ku ukashole, mowonekeratu kumadera a kwawo komweko komanso mochuluka kumaiko ena. Iyi ndi imodzi mwanjira zimene, momwe tidaganizira, zikuonetsa mzimu wa kuthandizana omwe ukuonetsedwa ndi abwenzi konse-konse. Mbumba zomwe mphamvu zamangidwa zadzipereka kuthandiza kupita chitsogolo komwe kukuchitika malo osiyana— mum’kwamba, m’chigawo, m’dziko angakhalenso mukontinenti—ndipo njira zaluso zapezeka zoperekera chilimbikitso kuchokera m’tali-m’tali ndikulora kuphunzira kuti kufale mwachindunji. Panopa, njira zosonkhanitsira pamodzi zophunziridwa mu mkwamba, kuti zithandizire kupanga mapulani kudera ndi kwina kulikonse, zikugwiritsidwa ntchito. Takhala okhutitsidwa kuona kuti chidwi chapadera chikuyikidwa pa kuphunzira zamomwe machitidwe apamwamba pa nkhani ya maphunziro a insitichuti kungapitire patsogolo. Pomwe maphunziro a insitichuti akhazikika m’dera zotsatira zake ndi zowonekeratu. Mwachitsanzo, umboni ndi kumalo kumene kukuchitika zochita-chita zakathithi komwe anthu ake atenga maphunziro a insitichuti kuti ndi chida chawo champhamvu: chida chimene chitukuko chake achitenga kukhala udindo wawo waukulu. Pozindikira kuti makomo a Chipembedzo amakhala otsegula nthawi zonse, okhulupilira akuphunzira momwe angaperekere chirimbikitso kwa iwo amene ali okonzeka kulowa. Kuyenda ndi mizimu yotereyi, ndikuyithandiza kuwoloka malire, ndimwayi komanso chisangalaro chapadera; muchikhalidwe chiri-chonse, pali zambiri zoti ziphunziridwe zokhudza nthawi iyi yakuzindikira ndi kukhala kumbali yake. Ndipo sizokhazi. Pomwe m’mikwamba yochuluka kuyesetsa kusonkhera ku ntchito zachitukuko kuli m’ndime zake zoyambilira, Mabungwe Auzimu Akulu, mothandizidwa bwino ndi Alangizi, akuyetsetsa kuphunzira zambiri momwe kuyetsetsa kumeneku kukutulukira kuchokera mu ndondomeko yomanga-mbumba. Zokambirana zokhuza ubwino wachitukuko chakuthupi cha anthu zikufukulidwa m’magulu am’maŵanja ndi mbumba, pomwe abwenzi akupezanso njira zomwe angatengere mbali m’zokambirana zatanthauzo zomwe zikuyamba kutambasuka m’madera owazungulira.
Pa zonse zimene tafotokoza, ntchito za achinyamata zikuwala mochititsa chidwi. Posakhala ongolandira chabe zotsatira—kaya zabwino kapena ayi—iwo awonetsa kuti ndi atenga-mbali a Pulani olimba mtima ndi ozindikira. Kumene mbumba yawaona iwowa mu chilinganizo ichi ndikuyika njira zowapititsira chitsogolo, achinyamatawa awonetsa kuchilimika kwawo. Iwo akuphunzitsa Chipembedzo kwa anzawo ndikupanga kutumikira kukhala maziko a maubwenzi a tanthauzo. Nthawi zambiri, kutumikira monga uku kukumakhala kuphunzitsa iwo amene ali achichepere kwaiwo—kuwapatsa iwo osati maphunziro akuthupi ndi kuuzimu kokha, komanso kuwathandizira pa maphunziro awo akusukulunso. Odzozedwa ndi udindo wopatulika wolimbitsa ndondomeko yainsitichuti, achinyamata achiBahá’í akukwanilitsa ziyembekezo zathu.
Kuyetsetsa konseku kukuchitikira mu dziko lampungwe-pungweli. Kuli konse kwavomerezeka kuti nsichi zadziko lapansi zagweduka ndipo sizingathenso kuchirikiza zosowekera za mtundu wa anthu tsopano. Zambiri zimene zimaoneka ngati zotsimikizika ndi zosatekeseka tsopano zikukayikitsa, ndipo zotsatira zake zikubweretsa kufunitsitsa kokhala ndi masomphenya amodzi. Mavume ovomereza umodzi, kukhala ndi mwayi ofanana, komanso chilungamo zikuonetsa kuchuluka kwa anthu omwe akufunira izi madera awo. Inde, sizodabwitsa kwawotsatira wa Wokongola Wodalitsika kuti mitima ifunitsitse mfundo zauzimu zimene Iye anaziphunzitsa. Ndichochititsa chidwi kuti m’chaka chimene mtundu wa anthu uli ndi chiyembekezo chopitira limodzi chitsogolo sikokayikitsayi, kuwala kwa Chipembedzo kwathwanima m’misonkhano yoposa mazana khumi (10,000) komwe anthu pafupi-fupi chikwi chimodzi ndi theka (1,500,000) amazukuta njira zopititsira mtsogolo mfundozi. Masomphenya ndilangizo la Bahá’u’lláh kumtundu waanthu kugwira ntchito mu umodzi wa ubwino wadziko lapansi, linali phata limene mbali zosiyana-siyana zadera zinasonkhanira mwachidwi—n’chifukwa chake, momwe wafotokozera ‘Abdu’l-Bahá, “mbumba ina ili yonse padziko lapansi ikupeza kuzindikira mu Ziphunzitso izi Zoyera kwamasomphenya ake apamwamba.” Anthu ena akufuna kwabwino poyambilira akhoza kuyitanidwira kumbumba yachiBaha’i ngati kumalo komwe angapeze chitetezo, mthunzi kudziko la tsankho ndi laulumali. Kuposera apa, zomwe akumapeza ndimizimu yaubwenzi yomwe ikugwilira ntchito limodzi kumanga dziko latsopano.
Zambiri zikanatha kulembedwa zokhuza kufalikira kwamisonkhano, mphamvu zapamwamba zomwe inapereka ku Pulani yatsopano, kapena chikondwelero chapansi pa mtima ndikuchilimika komwe inatulutsa mwaiwo amene anakhalanawo pa misonkhanoyo. Koma ndimawu ochepa awa tifuna kupereka chidwi chathu kuchimene chinaonedwa pa kupita mtsogolo kwa Chipembedzo. Inali kalilore wambumba yachiBahá’í imene imaona ubale, osati kusiyana. Ichi chinapangitsa ntchito yozukuta Pulani ya Zaka Zisanu ndi Zinayi kukhala yosavuta pamisonkhano imene anthu onse anali olandiridwa. Abwenzi analingalira zotsatira za Pulaniyi kumadera awo osati ndi mawanja awo okha ayi koma limodzi ndi atsogoleri akudera ndi enanso am’maudindo. Kubweretsa pamodzi anthu ochuluka kunapezetsa mwayi wokambirana mosinthika pankhani zakupita patsogolo kuzauzimu ndi zakuthupi, zimene zikutambasuka padziko lonse. Kusonkhera kwapadera kumene misonkhano imeneyi– imene onse anali olandiridwa, yosuntha komanso yacholinga–kungabweretse kachitidwe kotambasuka kopita m’tsogolo kwambumba mu mkwamba ndiphunziro lalikulu kuzikhadzikitso zachiBahá’í kuti ziringalire mtsogolo muno.
Ndipo tsopano mbumba yaokhulupirika ikulowa m’chaka chachiwiri cha Pulani ndikaganizidwe katsopano ndi kamvetsedwe kozama pa kufunikira kwachimene akuyenera kukwaniritsa. M’mene ntchito zosiyana-siyana zimaonekera poziyang’anira mphamvu zomanga dera zomwe zimatulutsa! Kutambasuka kwa masomphenya uku kukulora ntchito yopitilira kuti iwoneke kwambiri kusiyana ndi nchito yapayokha yakutumikira kapenanso ngati pongotolera chiwerengero. Dera ndi dera, ntchito zomwe zikuchitika zikuvumbula gulu la anthu lomwe likuphunzira kutenga udindo wochuluka kufufuza njira yachitukuko chawo chomwe.
Zotsatira zakusinthika kuuzimu komanso kuthupi zikuoneka zokha m’moyo waanthu munjira zosiyana-siyana. Mu m’ndandanda wa Mapulani apitawo, zolinga zimaonekeratu mu kupititsa patsogolo kwamaphunziro auzimu ndi kupembedza kwapamodzi. Mu m’ndandanda watsopano wa Mapulani, chidwi chowonjezereka chifunika chiperekedwe kundondomeko zina zimene zikufunika pakutukula moyo wambumba—mwachitsanzo, popititsa patsogolo nkhani zaumoyo waonse, kuteteza zachilengedwe, komanso kuchilimika pa mphamvu zamaluso. Chimene chikufunika kumbali zonse zowonjezera zaubwino wambumba kuti zipite patsogolo ndi, indetu, kuthekera kopanga kuphunzira kwandondomeko m’mbali zonsezi—kuthekera kumene kukutsamira pakuphunzira kochokera mu Ziphunzitso ndi kunkhokwe zanzeru za anthu zopezeka kuchokera ku ukadaulo wasayansi. Pomwe kuthekera uku kukukula, zambirizi zidzakwaniritsidwa m’zaka zomwe zikubwerazi.
Masomphenya awa otambasuka, omanga dera ali ndizotsatira zapatali. Mbumba ili yonse ili panjira yakeyake yokwaniritsa ichi. Koma kupita patsogolo kwa malo amodzi nthawi zambiri kumakhala ndi zina zofanana ndikupita patsogolo kwa malo ena. Chinthu chimodzi ndi chakuti, pomwe kuthekera kukuonjezereka ndipo mphamvu zambumba yadera kapena dziko zikuchulukira, kenako, m’kupita kwa nthawi, kufunikira kokhala ndi Nyumba Zopembedzeramo (Mashriqu’l-Adhkár), zomwe tinakamba kale mu uthenga wathu wa Riziwani 2012, zidzayamba kukwaniritsidwa. Momwe tinafotokozera mu uthenga wathu kwa inu wa Riziwani yathayi, nthawi ndi nthawi tidzisankha malo kumene Kachisi wachiBaha’i akuyenera kumangidwa. Ndife okondwa kulengeza, panthawi ino, kukhazikitsidwa kwa Nyumba Yopembedzeramo ku Kanchanpur, ku Nepal, ndiku Mwinilunga, ku Zambia. Kuwonjezera apa, tikulengezanso kuti Nyumba Yopembedzera yam’dziko imangidwe ku Canada, kudera lowandikana ndikomwe kuli likulu la Bungwe Lauzimu kuToronto. Ntchito zimenezi, ndizina zomwe zichitike mtsogolo muno, zizapindula ndithandizo loperekedwa ku Thumba la Nyumba Zopembedzera lomwe abwenzi padziko lonse amasonkhera.
Ochuluka ndi madalitso amene Ambuye wopereka ndi wachifundo wasankha kupereka kwa okondedwa Ake. Kwachiyero ndikuyitana, kukwezeka ndiwo masomphenya. Yofunikira kwambiri ndinthawi imene tonse tayitanidwa kuti titumikire. Kuchokera pansi pamtima, choncho, ndimapemphero amene, m’malo mwanu ndikuyesetsa kwanu kosatopa, tikupempherani pa Mapazi aBahá’u’lláh.
Inde, patangotsala chaka chimodzi kuti tikwangule ndime yoyamba ya Ndondomeko ya Zaka Zisanu ndi Zinayi, ndife okondwa kupereka tsatane-tsatane wa momwe ndondomekoyi ikuyendera—kubzolera m’zitsanzo zowala za kuyesetsa kwangwiro, zomwe Chipembedzochi chikuperekera masomphenya ndikudzadza mitima yochuluka ndi chiyembekezo.
Ndondomeko ya kukula ikupitira kupita patsogolo. Kubooleza kooneka kwachitika m’malo osiyana-siyana, kumene sikunachitikepo m’mbuyomu, komwe mbewu ya Chipembedzo tsopano yapatsa nthambi zatsopano zanthete ndipo kuthekera kogwira ntchito ndi mizimu yochuluka nthawi imodzi kwayamba kuwoneka. Kupita patsogolo uku kukutheka chifukwa cha mapayoniya odzipereka amene, ndimitima yoyatsidwa ndichikondi cha Mbuye wawo, achita machawi kukatumikira kwawo ngakhalenso kumaiko ena mwaunyinji ochititsa kaso. M’mikwamba momwe ndondomeko ya kukula inayamba kale, chidwi chatsopano chapatsidwa pa kugwiritsa ntchito, mwaluso ndi ukadaulo, njira zomwe zodziwika ndi m’ndandanda wa zochita zimene zipangitse abwenzi kudutsa mtunda wachiwiri ndi wachitatu. Ndipo mikwamba yamphamvu zoonekeratu, chithunzi champhamvu chomanga dera chachiChipembedzo chayamba kuoneka, pomwe patani yamphamvu ndi yosintha ya moyo wachiBahá’í ikuwonekera mu chiwerengero chochuluka cha mizimu yotsisimutsidwa.
Padakali pano, kukambirana ndi magulu am’dera kwapita patsogolo. Ntchito zam’madera zokhuza maphunziro zachulukana mofulumira kwambiri, komanso ntchito zina zapitanso patsogolo, monga zaulimi, zaumoyo, zachilengedwe, zopereka mphamvu kwa amayi komanso zaluso. Kupita patsogolo uku kukuwoneka kwambiri m’mikwamba yamphamvu kwambiri, kumene mudzi kapena dera—ngakhale m’ndandanda wa nyumba zingapo zondondozana kapena nyumba zakathithi—ndi kwawo kwa gulu lomwe likuona kutukuka komwe kumadza pakuyika mfundo zaChipembedzo muchikhalidwe chawo. M’malo ena, atsogoleri a dera pamodzi ndi iwo amene ali ndi udindo owona zamaphunziro a wana kapena chitukuko cham’dera sakungobwera kwa aBahá’í kuzafunsa nzeru kokha, koma akumafunanso kugwilira limodzi ntchito pofuna kupeza mayankho othekera. Kuwonjezera apo, ndife osangalala kuwona kuti pamlingo wadera komanso wadziko lonse, kachitidwe ndi kaganizidwe kachiBahá’í ku zokambirana zina zofunikira kukufuya kusililidwa ndi kuganiziridwa.
Chikonzero cha Zaka Zisanu ndi Zinayi chikudalira ndithu, pandondomeko ya dziko yophunzira zimene zili zopindulitsa m’madera aku Bolivia monga kuliri madera ena aku Sydney. Ndondomeko yakuphunzilirayi yabweretsa njira ndi machitidwe ogwirizana ndi dera lina lililonse. Ndiyadongosolo; ndiyosakakamiza; ndiyaponse-ponse. Ikubweretsa kulumikizana, kodzetsa maubale osiyana-siyana, pakati pa mawanja, pakati paokhala mowandikana, pakati pa achinyamata, komanso pakati pa onse omwe akonzeka kukhala atenga mbali mu ntchito yonyaditsayi. Imawutsa mbumba zosefukira ndikuthekera. Imalora kukwaniritsa maloto apamwamba omwe anthu omwe anasiyanitsidwa ndi malo, chiyankhulo, chikhalidwe, kapena zinthu zina koma tsopano amva ndi kuvomera kuyitana kwa Bahá’u’lláh kwa aliyense kuti “tiyesetse mosalekeza kutukula miyoyo ya wina ndi mnzake”. Ndipo zikudalira kotheratu pakuthekera kosalekeza kwa Liu la Mulungu— “mphamvu yoluzanitsa” ija, “yosuntha mizimu ndi yakuluzanitsa ndikubweretsa dongosolo m’dziko la umunthu”—ndipo pantchito yopitilira imapereka chilimbikitso.
Muchifwirimbiti cha thambo la m’dima, tawonani kuwala kothwanima kukuchokera mu kuyesesa kwakudzipereka kwanu! Ngakhale mkwiyo ukutsotsomoka m’dzikoli, thambo lomwe lidzakute mtundu wa anthu likumangidwa m’maiko, m’zigawo, ndi m’mikwamba. Koma zofunika kuchita ndizambiri. Mbumba iliyonse yam’dziko ili ndi chiyembekezo chake pakupita patsogolo komwe kukuyenera kuchitike mu ndime iyi, ndime yotsegulira Chikonzerochi. Nthawi ikupita. Abwenzi okondedwa, ndi ofalisa ziphunzitso zoyera, ndi achipambano a Wokongola Wodalitsika—kuyesetsa kwanu kukufunika pano. Kupita patsogolo kulikonse kumene kungachitike m'miyezi yolunjika ku Rizwáni akubwerayu kudzapereka mangolomera ku mbumba ya Dzina Lalikulu ku zimene iyenera kukwaniritsa mu ndime yachiwiri ya Chikonzerochi. Mulandire chipambano. Pa ichi tikupempha Ambuye wokwezeka; pa ichi tikupempha thandizo Lake losalephera; pa ichi tipemha Ambuye atumize angelo Ake okondedwa kuti athandize aliyense wa inu.